< Masalimo 115 >

1 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi koma ulemerero ukhale pa dzina lanu, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
Not to us, LORD, not to us, but to your name be the glory, for your loving kindness and for your faithfulness.
2 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti, “Mulungu wawo ali kuti?”
Why should the nations say, "Where is their God, now?"
3 Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
But our God is in the heavens. He does whatever he pleases.
4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
Their idols are silver and gold, the work of men's hands.
5 Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya;
They have mouths, but they do not speak. They have eyes, but they do not see.
6 makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
They have ears, but they do not hear. They have noses, but they do not smell.
7 manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
They have hands, but they do not feel. They have feet, but they do not walk, neither do they speak through their throat.
8 Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
Those who make them will be like them; yes, everyone who trusts in them.
9 Inu Aisraeli, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
Israel, trust in the LORD. He is their help and their shield.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova; Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
House of Aaron, trust in the LORD. He is their help and their shield.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
You who fear the LORD, trust in the LORD. He is their help and their shield.
12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israeli, adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
The LORD remembers us. He will bless us. He will bless the house of Israel. He will bless the house of Aaron.
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova; aangʼono ndi aakulu omwe.
He will bless those who fear the LORD, both small and great.
14 Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu.
May the LORD increase you more and more, you and your children.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Blessed are you by the LORD, who made heaven and earth.
16 Kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
The heavens are the heavens of the LORD; but the earth has he given to the descendants of Adam.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova, amene amatsikira kuli chete;
The dead do not praise the LORD, neither any who go down into silence;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova, kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Yehova.
But we will bless the LORD, from this time forth and forevermore. Praise the LORD.

< Masalimo 115 >