< Masalimo 114 >

1 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
בְּצֵ֣את יִ֭שְׂרָאֵל מִמִּצְרָ֑יִם בֵּ֥ית יַ֝עֲקֹ֗ב מֵעַ֥ם לֹעֵֽז׃
2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake.
הָיְתָ֣ה יְהוּדָ֣ה לְקָדְשׁ֑וֹ יִ֝שְׂרָאֵ֗ל מַמְשְׁלוֹתָֽיו׃
3 Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
הַיָּ֣ם רָ֭אָה וַיָּנֹ֑ס הַ֝יַּרְדֵּ֗ן יִסֹּ֥ב לְאָחֽוֹר׃
4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa.
הֶֽ֭הָרִים רָקְד֣וּ כְאֵילִ֑ים גְּ֝בָע֗וֹת כִּבְנֵי־צֹֽאן׃
5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa? iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
מַה־לְּךָ֣ הַ֭יָּם כִּ֣י תָנ֑וּס הַ֝יַּרְדֵּ֗ן תִּסֹּ֥ב לְאָחֽוֹר׃
6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna, inu timapiri, ngati ana ankhosa?
הֶֽ֭הָרִים תִּרְקְד֣וּ כְאֵילִ֑ים גְּ֝בָע֗וֹת כִּבְנֵי־צֹֽאן׃
7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi, pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
מִלִּפְנֵ֣י אָ֭דוֹן ח֣וּלִי אָ֑רֶץ מִ֝לִּפְנֵ֗י אֱל֣וֹהַּ יַעֲקֹֽב׃
8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime, thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.
הַהֹפְכִ֣י הַצּ֣וּר אֲגַם־מָ֑יִם חַ֝לָּמִ֗ישׁ לְמַעְיְנוֹ־מָֽיִם ׃

< Masalimo 114 >