< Masalimo 110 >

1 Salimo la Davide. Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.”
A Psalm of David. The LORD saith unto my lord: 'Sit thou at My right hand, until I make thine enemies thy footstool.'
2 Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako.
The rod of Thy strength the LORD will send out of Zion: 'Rule thou in the midst of thine enemies.'
3 Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako.
Thy people offer themselves willingly in the day of thy warfare; in adornments of holiness, from the womb of the dawn, thine is the dew of thy youth.
4 Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake: “Ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
The LORD hath sworn, and will not repent: 'Thou art a priest for ever after the manner of Melchizedek.'
5 Ambuye ali kudzanja lako lamanja; Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.
The Lord at thy right hand doth crush kings in the day of His wrath.
6 Adzaweruza anthu a mitundu ina, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.
He will judge among the nations; He filleth it with dead bodies, He crusheth the head over a wide land.
7 Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira; choncho adzaweramutsa mutu wake.
He will drink of the brook in the way; therefore will he lift up the head.

< Masalimo 110 >