< Masalimo 11 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame.
In the LORD put I my trust: how say all of you to my soul, Flee as a bird to your mountain?
2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima.
For, lo, the wicked bend their bow, they make ready their arrow upon the string, that they may privately shoot at the upright in heart.
3 Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?”
If the foundations be destroyed, what can the righteous do?
4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.
The LORD is in his holy temple, the LORD's throne is in heaven: his eyes behold, his eyelids try, the children of men.
5 Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa.
The LORD tries the righteous: but the wicked and him that loves violence his soul hates.
6 Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera.
Upon the wicked he shall rain snares, fire and brimstone, and an horrible tempest: this shall be the portion of their cup.
7 Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.
For the righteous LORD loves righteousness; his countenance does behold the upright.

< Masalimo 11 >