< Masalimo 109 >

1 Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Salimo la Davide. Mulungu amene ndimakutamandani, musakhale chete,
聖歌隊の指揮者によってうたわせたダビデの歌 わたしのほめたたえる神よ、もださないでください。
2 pakuti anthu oyipa ndi achinyengo atsekula pakamwa pawo kutsutsana nane; iwo ayankhula motsutsana nane ndi malilime abodza.
彼らは悪しき口と欺きの口をあけて、わたしにむかい、偽りの舌をもってわたしに語り、
3 Andizungulira ndi mawu audani, amandinena popanda chifukwa.
恨みの言葉をもってわたしを囲み、ゆえなくわたしを攻めるのです。
4 Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza, koma ine ndine munthu wapemphero.
彼らはわが愛にむくいて、わたしを非難します。しかしわたしは彼らのために祈ります。
5 Iwo amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino, ndi udani mʼmalo mwa chikondi changa.
彼らは悪をもってわが善に報い、恨みをもってわが愛に報いるのです。
6 Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye; lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja.
彼の上に悪しき人を立て、訴える者に彼を訴えさせてください。
7 Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa, ndipo mapemphero ake amutsutse.
彼がさばかれるとき、彼を罪ある者とし、その祈を罪に変えてください。
8 Masiku ake akhale owerengeka; munthu wina atenge malo ake a utsogoleri.
その日を少なくし、その財産をほかの人にとらせ、
9 Ana ake akhale amasiye ndipo mkazi wake akhale wopanda mwamuna.
その子らをみなしごにし、その妻をやもめにしてください。
10 Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha; apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.
その子らを放浪者として施しをこわせ、その荒れたすまいから追い出させてください。
11 Wokongoza alande zonse zimene ali nazo; alendo afunkhe ntchito za manja ake.
彼が持っているすべての物を債主に奪わせ、その勤労の実をほかの人にかすめさせてください。
12 Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.
彼にいつくしみを施す者はひとりもなく、またそのみなしごをあわれむ者もなく、
13 Zidzukulu zake zithe nʼkufa, mayina awo afafanizidwe mu mʼbado wotsatirawo.
その子孫を絶えさせ、その名を次の代に消し去ってください。
14 Mphulupulu za makolo ake zikumbukiridwe pamaso pa Yehova; tchimo la amayi ake lisadzafafanizidwe.
その父たちの不義は主のみ前に覚えられ、その母の罪を消し去らないでください。
15 Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse, kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi.
それらを常に主のみ前に置き、彼の記憶を地から断ってください。
16 Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo, koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka ndi osweka mtima.
これは彼がいつくしみを施すことを思わず、かえって貧しい者、乏しい者を責め、心の痛める者を殺そうとしたからです。
17 Anakonda kutemberera, matembererowo abwerere kwa iye; sanakondwe nʼkudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali naye.
彼はのろうことを好んだ。のろいを彼に臨ませてください。彼は恵むことを喜ばなかった。恵みを彼から遠ざけてください。
18 Anavala kutemberera ngati chovala; kutemberera kunalowa mʼthupi lake ngati madzi, kulowa mʼmafupa ake ngati mafuta.
彼はのろいを衣のように着た。のろいを水のようにその身にしみこませ、油のようにその骨にしみこませてください。
19 Matemberero akhale ngati chofunda chodzikutira nacho, ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.
またそれを自分の着る着物のようにならせ、常に締める帯のようにならせてください。
20 Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga, kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.
これがわたしを非難する者と、わたしに逆らって悪いことを言う者の主からうける報いとしてください。
21 Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse, muchite nane molingana ndi dzina lanu, chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.
しかし、わが主なる神よ、あなたはみ名のために、わたしを顧みてください。あなたのいつくしみの深きにより、わたしをお助けください。
22 Pakuti ndine wosauka ndi wosowa, ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga.
わたしは貧しく、かつ乏しいのです。わたしの心はわがうちに傷ついています。
23 Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.
わたしは夕日の影のように去りゆき、いなごのように追い払われます。
24 Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya, thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.
わたしのひざは断食によってよろめき、わたしの肉はやせ衰え、
25 Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane; akandiona, amapukusa mitu yawo.
わたしは彼らにそしられる者となりました。彼らはわたしを見ると、頭を振ります。
26 Thandizeni Inu Yehova Mulungu wanga; pulumutseni molingana ndi chikondi chanu.
わが神、主よ、わたしをお助けください。あなたのいつくしみにしたがって、わたしをお救いください。
27 Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu, kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.
主よ、これがあなたのみ手のわざであること、あなたがそれをなされたことを、彼らに知らせてください。
28 Angathe kutemberera, koma Inu mudzadalitsa; pamene iwo andiputa adzachititsidwa manyazi, koma mtumiki wanu adzasangalala.
彼らはのろうけれども、あなたは祝福されます。わたしを攻める者をはずかしめ、あなたのしもべを喜ばせてください。
29 Onditsutsa adzavekedwa mnyozo, ndipo adzadzifunditsa manyazi ngati chovala.
わたしを非難する者にはずかしめを着せ、おのが恥を上着のようにまとわせてください。
30 Ndi pakamwa panga ndidzathokoza Yehova kwambiri; ndidzamutamanda mʼgulu lalikulu la anthu.
わたしはわが口をもって大いに主に感謝し、多くの人のなかで主をほめたたえます。
31 Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo, kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.
主は貧しい者の右に立って、死罪にさだめようとする者から彼を救われるからです。

< Masalimo 109 >