< Masalimo 108 >

1 Nyimbo. Salimo la Davide. Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu; ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.
A Song. A Psalm by David. My heart is steadfast, God. I will sing and I will make music with my soul.
2 Dzukani, zeze ndi pangwe! Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.
Wake up, harp and lyre! I will wake up the dawn.
3 Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.
I will give thanks to you, LORD, amongst the nations. I will sing praises to you amongst the peoples.
4 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba; kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.
For your loving kindness is great above the heavens. Your faithfulness reaches to the skies.
5 Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba, ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.
Be exalted, God, above the heavens! Let your glory be over all the earth.
6 Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
That your beloved may be delivered, save with your right hand, and answer us.
7 Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.
God has spoken from his sanctuary: “In triumph, I will divide Shechem, and measure out the valley of Succoth.
8 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.
Gilead is mine. Manasseh is mine. Ephraim also is my helmet. Judah is my sceptre.
9 Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu; ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”
Moab is my wash pot. I will toss my sandal on Edom. I will shout over Philistia.”
10 Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
Who will bring me into the fortified city? Who will lead me to Edom?
11 Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?
Haven’t you rejected us, God? You don’t go out, God, with our armies.
12 Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani, pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.
Give us help against the enemy, for the help of man is vain.
13 Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano, ndipo adzapondereza pansi adani athu.
Through God, we will do valiantly, for it is he who will tread down our enemies.

< Masalimo 108 >