< Masalimo 107 >
1 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Preiset Jehova, denn er ist gut, denn seine Güte währt ewiglich!
2 Owomboledwa a Yehova anene zimenezi amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
So sollen sagen die Erlösten Jehovas, die er aus der Hand des Bedrängers erlöst,
3 iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko, kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
und die er gesammelt hat aus den Ländern, von Osten und von Westen, von Norden und vom Meere.
4 Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu, osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.
Sie irrten umher in der Wüste, auf ödem Wege, sie fanden keine Wohnstadt.
5 Iwo anamva njala ndi ludzu, ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.
Hungrig waren sie und durstig, es verschmachtete in ihnen ihre Seele.
6 Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
Da schrieen sie zu Jehova in ihrer Bedrängnis, und aus ihren Drangsalen errettete er sie.
7 Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.
Und er leitete sie auf rechtem Wege, daß sie zu einer Wohnstadt gelangten.
8 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
Mögen sie Jehova preisen wegen seiner Güte und wegen seiner Wundertaten an den Menschenkindern!
9 pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.
Denn er hat die durstende Seele gesättigt und die hungernde Seele mit Gutem erfüllt.
10 Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu, amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,
Die Bewohner der Finsternis und des Todesschattens, gefesselt in Elend und Eisen:
11 pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.
Weil sie widerspenstig gewesen waren gegen die Worte Gottes und verachtet hatten den Rat des Höchsten,
12 Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga; anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.
so beugte er ihr Herz durch Mühsal; sie strauchelten, und kein Helfer war da.
13 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
Da schrieen sie zu Jehova in ihrer Bedrängnis, und aus ihren Drangsalen rettete er sie.
14 Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu ndipo anadula maunyolo awo.
Er führte sie heraus aus der Finsternis und dem Todesschatten, und zerriß ihre Fesseln.
15 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
Mögen sie Jehova preisen wegen seiner Güte und wegen seiner Wundertaten an den Menschenkindern!
16 pakuti Iye amathyola zipata zamkuwa ndi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.
Denn er hat zerbrochen die ehernen Türen und die eisernen Riegel zerschlagen.
17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira, ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
Die Toren leiden ob des Weges ihrer Übertretung und ob ihrer Ungerechtigkeiten.
18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
Ihre Seele verabscheut jede Speise, und sie kommen bis an die Pforten des Todes.
19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
Dann schreien sie zu Jehova in ihrer Bedrängnis, und aus ihren Drangsalen rettet er sie.
20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa; anawalanditsa ku manda.
Er sendet sein Wort und heilt sie, und er errettet sie aus ihren Gruben.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
Mögen sie Jehova preisen wegen seiner Güte und wegen seiner Wundertaten an den Menschenkindern;
22 Apereke nsembe yachiyamiko ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
und Opfer des Lobes opfern und mit Jubel erzählen seine Taten!
23 Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi; Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.
Die sich auf Schiffen aufs Meer hinabbegeben, auf großen Wassern Handel treiben,
24 Anaona ntchito za Yehova, machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.
diese sehen die Taten Jehovas und seine Wunderwerke in der Tiefe:
25 Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkuntho imene inabweretsa mafunde ataliatali.
Er spricht und bestellt einen Sturmwind, der hoch erhebt seine Wellen.
26 Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya; pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.
Sie fahren hinauf zum Himmel, sinken hinab in die Tiefen; es zerschmilzt in der Not ihre Seele.
27 Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera; anali pa mapeto a moyo wawo.
Sie taumeln und schwanken wie ein Trunkener, und zunichte wird alle ihre Weisheit.
28 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.
Dann schreien sie zu Jehova in ihrer Bedrängnis, und er führt sie heraus aus ihren Drangsalen.
29 Yehova analetsa namondwe, mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.
Er verwandelt den Sturm in Stille, und es legen sich die Wellen.
30 Anali osangalala pamene kunakhala bata, ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.
Und sie freuen sich, daß sie sich beruhigen, und er führt sie in den ersehnten Hafen.
31 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
Mögen sie Jehova preisen wegen seiner Güte, und wegen seiner Wundertaten an den Menschenkindern.
32 Akuze Iye mu msonkhano wa anthu ndi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.
Und ihn erheben in der Versammlung des Volkes, und in der Sitzung der Ältesten ihn loben!
33 Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu, akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,
Er macht Ströme zur Wüste und Wasserquellen zu dürrem Lande,
34 ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere, chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.
fruchtbares Land zur Salzsteppe wegen der Bosheit der darin Wohnenden.
35 Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;
Er macht zum Wasserteich die Wüste und dürres Land zu Wasserquellen;
36 kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako, ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.
und er läßt Hungrige daselbst wohnen und sie gründen eine Wohnstadt.
37 Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa ndipo anakolola zipatso zochuluka;
Und sie besäen Felder und pflanzen Weinberge, welche Frucht bringen als Ertrag;
38 Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri, ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.
und er segnet sie, und sie mehren sich sehr, und ihres Viehes läßt er nicht wenig sein.
39 Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwa chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;
Und sie vermindern sich und werden gebeugt durch Bedrückung, Unglück und Jammer.
40 Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezeka anawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.
Er schüttet Verachtung auf Fürsten, und läßt sie umherirren in pfadloser Einöde;
41 Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awo ngati magulu a nkhosa.
und er hebt den Armen empor aus dem Elend, und macht Herden gleich seine Geschlechter.
42 Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala, koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.
Die Aufrichtigen werden es sehen und sich freuen, und alle Ungerechtigkeit wird ihren Mund verschließen.
43 Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezi ndi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.
Wer weise ist, der wird dieses beachten, und verstehen werden sie die Gütigkeiten Jehovas.