< Masalimo 106 >
1 Tamandani Yehova. Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova kapena kumutamanda mokwanira?
3 Odala ndi amene amasunga chilungamo, amene amachita zolungama nthawi zonse.
4 Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu, bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
5 kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika, kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.
6 Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu; tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
7 Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
8 Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
9 Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma; anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10 Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo; anawawombola mʼdzanja la mdani.
11 Madzi anamiza adani awo, palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12 Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake ndi kuyimba nyimbo zamatamando.
13 Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake.
14 Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.
15 Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa.
16 Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni, amene Yehova anadzipatulira.
17 Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani; inakwirira gulu la Abiramu.
18 Moto unayaka pakati pa otsatira awo; lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.
19 Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20 Anasinthanitsa ulemerero wawo ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21 Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa, amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22 zozizwitsa mʼdziko la Hamu ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23 Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga, pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa, kuyima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.
24 Motero iwo ananyoza dziko lokoma; sanakhulupirire malonjezo ake.
25 Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo ndipo sanamvere Yehova.
26 Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake, kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,
27 kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.
28 Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;
29 anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa, ndipo mliri unabuka pakati pawo.
30 Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo, ndipo mliri unaleka.
31 Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake, kwa mibado yosatha imene ikubwera.
32 Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,
33 pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu, ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.
34 Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu monga momwe Yehova anawalamulira.
35 Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo ndi kuphunzira miyambo yawo.
36 Ndipo anapembedza mafano awo, amene anakhala msampha kwa iwowo.
37 Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.
38 Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
39 Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita; ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.
40 Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.
41 Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina, ndipo adani awo anawalamulira.
42 Adani awo anawazunza ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.
43 Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri, koma iwo ankatsimikiza za kuwukira ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.
44 Koma Iye anaona kuzunzika kwawo pamene anamva kulira kwawo;
45 Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.
46 Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo awamvere chisoni.
47 Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu, ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera ndi kunyadira mʼmatamando anu.
48 Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, Kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Ameni!” Tamandani Yehova.