< Masalimo 105 >

1 Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
הודו ליהוה קראו בשמו הודיעו בעמים עלילותיו׃
2 Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo; fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
שירו לו זמרו לו שיחו בכל נפלאותיו׃
3 Munyadire dzina lake loyera; mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
התהללו בשם קדשו ישמח לב מבקשי יהוה׃
4 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi yonse.
דרשו יהוה ועזו בקשו פניו תמיד׃
5 Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita, zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
זכרו נפלאותיו אשר עשה מפתיו ומשפטי פיו׃
6 inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake.
זרע אברהם עבדו בני יעקב בחיריו׃
7 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.
הוא יהוה אלהינו בכל הארץ משפטיו׃
8 Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya, mawu amene analamula kwa mibado yonse,
זכר לעולם בריתו דבר צוה לאלף דור׃
9 pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu, lumbiro limene analumbira kwa Isake.
אשר כרת את אברהם ושבועתו לישחק׃
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa, kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
ויעמידה ליעקב לחק לישראל ברית עולם׃
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani ngati gawo la cholowa chako.”
לאמר לך אתן את ארץ כנען חבל נחלתכם׃
12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero, ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
בהיותם מתי מספר כמעט וגרים בה׃
13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina, kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
ויתהלכו מגוי אל גוי מממלכה אל עם אחר׃
14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza; anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
לא הניח אדם לעשקם ויוכח עליהם מלכים׃
15 “Musakhudze odzozedwa anga; musachitire choyipa aneneri anga.”
אל תגעו במשיחי ולנביאי אל תרעו׃
16 Iye anabweretsa njala pa dziko ndipo anawononga chakudya chonse;
ויקרא רעב על הארץ כל מטה לחם שבר׃
17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo, Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
שלח לפניהם איש לעבד נמכר יוסף׃
18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza, khosi lake analiyika mʼzitsulo,
ענו בכבל רגליו ברזל באה נפשו׃
19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa, mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
עד עת בא דברו אמרת יהוה צרפתהו׃
20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula, wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
שלח מלך ויתירהו משל עמים ויפתחהו׃
21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake, wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
שמו אדון לביתו ומשל בכל קנינו׃
22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunira ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.
לאסר שריו בנפשו וזקניו יחכם׃
23 Tsono Israeli analowa mu Igupto; Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
ויבא ישראל מצרים ויעקב גר בארץ חם׃
24 Yehova anachulukitsa anthu ake; ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
ויפר את עמו מאד ויעצמהו מצריו׃
25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.
הפך לבם לשנא עמו להתנכל בעבדיו׃
26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
שלח משה עבדו אהרן אשר בחר בו׃
27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo, zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
שמו בם דברי אתותיו ומפתים בארץ חם׃
28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima. Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
שלח חשך ויחשך ולא מרו את דבריו׃
29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi, kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
הפך את מימיהם לדם וימת את דגתם׃
30 Dziko lawo linadzaza ndi achule amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
שרץ ארצם צפרדעים בחדרי מלכיהם׃
31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
אמר ויבא ערב כנים בכל גבולם׃
32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala, ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
נתן גשמיהם ברד אש להבות בארצם׃
33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu, nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
ויך גפנם ותאנתם וישבר עץ גבולם׃
34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera, ziwala zosawerengeka;
אמר ויבא ארבה וילק ואין מספר׃
35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo, zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
ויאכל כל עשב בארצם ויאכל פרי אדמתם׃
36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo, zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.
ויך כל בכור בארצם ראשית לכל אונם׃
37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri, ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
ויוציאם בכסף וזהב ואין בשבטיו כושל׃
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka, pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
שמח מצרים בצאתם כי נפל פחדם עליהם׃
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo, ndi moto owawunikira usiku.
פרש ענן למסך ואש להאיר לילה׃
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
שאל ויבא שלו ולחם שמים ישביעם׃
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka; ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.
פתח צור ויזובו מים הלכו בציות נהר׃
42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
כי זכר את דבר קדשו את אברהם עבדו׃
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera, osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
ויוצא עמו בששון ברנה את בחיריו׃
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
ויתן להם ארצות גוים ועמל לאמים יירשו׃
45 kuti iwo asunge malangizo ake ndi kutsatira malamulo ake. Tamandani Yehova.
בעבור ישמרו חקיו ותורתיו ינצרו הללו יה׃

< Masalimo 105 >