< Masalimo 104 >
1 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu.
ipsi David benedic anima mea Domino Domine Deus meus magnificatus es vehementer confessionem et decorem induisti
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti
amictus lumine sicut vestimento extendens caelum sicut pellem
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake. Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake, ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
qui tegis in aquis superiora eius qui ponis nubem ascensum tuum qui ambulas super pinnas ventorum
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake, malawi amoto kukhala atumiki ake.
qui facis angelos tuos spiritus et ministros tuos ignem urentem
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake; silingasunthike.
qui fundasti terram super stabilitatem suam non inclinabitur in saeculum saeculi
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala; madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
abyssus sicut vestimentum amictus eius super montes stabunt aquae
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa, pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
ab increpatione tua fugient a voce tonitrui tui formidabunt
8 Inu munamiza mapiri, iwo anatsikira ku zigwa kumalo kumene munawakonzera.
ascendunt montes et descendunt campi in locum quem fundasti eis
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa, iwo sadzamizanso dziko lapansi.
terminum posuisti quem non transgredientur neque convertentur operire terram
10 Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa; madziwo amayenda pakati pa mapiri.
qui emittis fontes in convallibus inter medium montium pertransibunt aquae
11 Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo; abulu akuthengo amapha ludzu lawo.
potabunt omnes bestiae agri expectabunt onagri in siti sua
12 Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi; zimayimba pakati pa thambo.
super ea volucres caeli habitabunt de medio petrarum dabunt vocem
13 Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba; dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.
rigans montes de superioribus suis de fructu operum tuorum satiabitur terra
14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye, ndi zomera, kuti munthu azilima kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:
producens faenum iumentis et herbam servituti hominum ut educas panem de terra
15 vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu, mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala, ndi buledi amene amapereka mphamvu.
et vinum laetificat cor hominis ut exhilaret faciem in oleo et panis cor hominis confirmat
16 Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino, mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.
saturabuntur ligna campi et cedri Libani quas plantavit
17 Mbalame zimamanga zisa zawo; kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.
illic passeres nidificabunt erodii domus dux est eorum
18 Mapiri ataliatali ndi a mbalale; mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.
montes excelsi cervis petra refugium erinaciis
19 Mwezi umasiyanitsa nyengo ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.
fecit lunam in tempora sol cognovit occasum suum
20 Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku, ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.
posuisti tenebras et facta est nox in ipsa pertransibunt omnes bestiae silvae
21 Mikango imabangula kufuna nyama, ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.
catuli leonum rugientes ut rapiant et quaerant a Deo escam sibi
22 Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala; imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.
ortus est sol et congregati sunt et in cubilibus suis conlocabuntur
23 Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake, kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.
exibit homo ad opus suum et ad operationem suam usque ad vesperum
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova! Munazipanga zonse mwanzeru, dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
quam magnificata sunt opera tua Domine omnia in sapientia fecisti impleta est terra possessione tua
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka, zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
hoc mare magnum et spatiosum manibus; illic reptilia quorum non est numerus animalia pusilla cum magnis
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku, ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.
illic naves pertransibunt draco iste quem formasti ad inludendum ei
27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
omnia a te expectant ut des illis escam in tempore
28 Mukazipatsa, zimachisonkhanitsa pamodzi; mukatsekula dzanja lanu, izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
dante te illis colligent aperiente te manum tuam omnia implebuntur bonitate
29 Mukabisa nkhope yanu, izo zimachita mantha aakulu; mukachotsa mpweya wawo, zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
avertente autem te faciem turbabuntur auferes spiritum eorum et deficient et in pulverem suum revertentur
30 Mukatumiza mzimu wanu, izo zimalengedwa ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.
emittes spiritum tuum et creabuntur et renovabis faciem terrae
31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya; Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
sit gloria Domini in saeculum laetabitur Dominus in operibus suis
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera, amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.
qui respicit terram et facit eam tremere qui tangit montes et fumigant
33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse; ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
cantabo Domino in vita mea psallam Deo meo quamdiu sum
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye, pamene ndikusangalala mwa Yehova.
iucundum sit ei eloquium meum ego vero delectabor in Domino
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi ndipo anthu oyipa asapezekenso. Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga. Tamandani Yehova.
deficiant peccatores a terra et iniqui ita ut non sint benedic anima mea Domino