< Masalimo 103 >

1 Salimo la Davide. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga; ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
לדוד ברכי נפשי את-יהוה וכל-קרבי את-שם קדשו
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
ברכי נפשי את-יהוה ואל-תשכחי כל-גמוליו
3 Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
הסלח לכל-עונכי הרפא לכל-תחלואיכי
4 amene awombola moyo wako ku dzenje ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
הגואל משחת חייכי המעטרכי חסד ורחמים
5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
המשביע בטוב עדיך תתחדש כנשר נעוריכי
6 Yehova amachita chilungamo ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
עשה צדקות יהוה ומשפטים לכל-עשוקים
7 Iye anadziwitsa Mose njira zake, ntchito zake kwa Aisraeli.
יודיע דרכיו למשה לבני ישראל עלילותיו
8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
רחום וחנון יהוה ארך אפים ורב-חסד
9 Iye sadzatsutsa nthawi zonse, kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
לא-לנצח יריב ולא לעולם יטור
10 satichitira molingana ndi machimo athu, kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
לא כחטאינו עשה לנו ולא כעונתינו גמל עלינו
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
כי כגבה שמים על-הארץ-- גבר חסדו על-יראיו
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
כרחק מזרח ממערב-- הרחיק ממנו את-פשעינו
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake, choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
כרחם אב על-בנים-- רחם יהוה על-יראיו
14 pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira, amakumbukira kuti ndife fumbi.
כי-הוא ידע יצרנו זכור כי-עפר אנחנו
15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu, amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
אנוש כחציר ימיו כציץ השדה כן יציץ
16 koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso ndipo malo ake sakumbukirikanso.
כי רוח עברה-בו ואיננו ולא-יכירנו עוד מקומו
17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
וחסד יהוה מעולם ועד-עולם-- על-יראיו וצדקתו לבני בנים
18 iwo amene amasunga pangano lake ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
לשמרי בריתו ולזכרי פקדיו לעשותם
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.
יהוה--בשמים הכין כסאו ומלכותו בכל משלה
20 Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake.
ברכו יהוה מלאכיו גברי כח עשי דברו לשמע בקול דברו
21 Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba, inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
ברכו יהוה כל-צבאיו-- משרתיו עשי רצונו
22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse kulikonse mu ulamuliro wake. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
ברכו יהוה כל-מעשיו-- בכל-מקמות ממשלתו ברכי נפשי את-יהוה

< Masalimo 103 >