< Masalimo 102 >

1 Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko. Yehova imvani pemphero langa; kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
תפלה לעני כי יעטף ולפני יהוה ישפך שיחו יהוה שמעה תפלתי ושועתי אליך תבוא׃
2 Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pa msautso. Munditcherere khutu; pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.
אל תסתר פניך ממני ביום צר לי הטה אלי אזנך ביום אקרא מהר ענני׃
3 Pakuti masiku anga akupita ngati utsi; mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
כי כלו בעשן ימי ועצמותי כמו קד נחרו׃
4 Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu; ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
הוכה כעשב ויבש לבי כי שכחתי מאכל לחמי׃
5 Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
מקול אנחתי דבקה עצמי לבשרי׃
6 Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu, monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
דמיתי לקאת מדבר הייתי ככוס חרבות׃
7 Ndimagona osapeza tulo; ndakhala ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
שקדתי ואהיה כצפור בודד על גג׃
8 Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe; iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
כל היום חרפוני אויבי מהוללי בי נשבעו׃
9 Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
כי אפר כלחם אכלתי ושקוי בבכי מסכתי׃
10 chifukwa cha ukali wanu waukulu, popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
מפני זעמך וקצפך כי נשאתני ותשליכני׃
11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo; Ine ndikufota ngati udzu.
ימי כצל נטוי ואני כעשב איבש׃
12 Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya; kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
ואתה יהוה לעולם תשב וזכרך לדר ודר׃
13 Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo; nthawi yoyikika yafika.
אתה תקום תרחם ציון כי עת לחננה כי בא מועד׃
14 Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu; fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
כי רצו עבדיך את אבניה ואת עפרה יחננו׃
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova, mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
וייראו גוים את שם יהוה וכל מלכי הארץ את כבודך׃
16 Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni ndi kuonekera mu ulemerero wake.
כי בנה יהוה ציון נראה בכבודו׃
17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.
פנה אל תפלת הערער ולא בזה את תפלתם׃
18 Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo, kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:
תכתב זאת לדור אחרון ועם נברא יהלל יה׃
19 “Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba, kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,
כי השקיף ממרום קדשו יהוה משמים אל ארץ הביט׃
20 kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende, kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”
לשמע אנקת אסיר לפתח בני תמותה׃
21 Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni ndi matamando ake mu Yerusalemu,
לספר בציון שם יהוה ותהלתו בירושלם׃
22 pamene mitundu ya anthu ndi maufumu adzasonkhana kuti alambire Yehova.
בהקבץ עמים יחדו וממלכות לעבד את יהוה׃
23 Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga; Iyeyo anafupikitsa masiku anga.
ענה בדרך כחו קצר ימי׃
24 Choncho Ine ndinati: “Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga; zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.
אמר אלי אל תעלני בחצי ימי בדור דורים שנותיך׃
25 Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.
לפנים הארץ יסדת ומעשה ידיך שמים׃
26 Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa.
המה יאבדו ואתה תעמד וכלם כבגד יבלו כלבוש תחליפם ויחלפו׃
27 Koma Inu simusintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.
ואתה הוא ושנותיך לא יתמו׃
28 Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu; zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”
בני עבדיך ישכונו וזרעם לפניך יכון׃

< Masalimo 102 >