< Masalimo 101 >

1 Salimo la Davide. Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
A Psalm. Of David. I will make a song of mercy and righteousness; to you, O Lord, will I make melody.
2 Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa.
I will do wisely in the way of righteousness: O when will you come to me? I will be walking in my house with a true heart.
3 Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa pamaso panga. Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; iwo sadzadziphatika kwa ine.
I will not put any evil thing before my eyes; I am against all turning to one side; I will not have it near me.
4 Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.
The false heart I will send away from me: I will not have an evil-doer for a friend.
5 Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.
I will put to death anyone who says evil of his neighbour secretly; the man with a high look and a heart of pride is disgusting to me.
6 Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira.
My eyes will be on those of good faith in the land, so that they may be living in my house; he who is walking in the right way will be my servant.
7 Aliyense wochita chinyengo sadzakhala mʼnyumba mwanga. Aliyense woyankhula mwachinyengo sadzayima pamaso panga.
The worker of deceit will not come into my house; the false man will have no place before my eyes.
8 Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu onse oyipa mʼdziko; ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa mu mzinda wa Yehova.
Morning by morning will I put to death all the sinners in the land, so that all evil-doers may be cut off from Jerusalem.

< Masalimo 101 >