< Masalimo 100 >

1 Salimo. Nyimbo yothokoza. Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
(감사의 시) 온 땅이여, 여호와께 즐거이 부를지어다
2 Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
기쁨으로 여호와를 섬기며 노래하면서 그 앞에 나아갈지어다
3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.
여호와가 우리 하나님이신 줄 너희는 알지어다! 그는 우리를 지으신 자시요 우리는 그의 것이니 그의 백성이요 그의 기르시는 양이로다
4 Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
감사함으로 그 문에 들어가며 찬송함으로 그 궁정에 들어가서 그에게 감사하며 그 이름을 송축할지어다
5 Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.
대저 여호와는 선하시니 그 인자하심이 영원하고 그 성실하심이 대대에 미치리로다

< Masalimo 100 >