< Miyambo 1 >
1 Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:
2 Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo; kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
3 kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru, akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
4 Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera, achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
5 Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake, ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
6 kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.
7 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
8 Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
9 Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
10 Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa usamawamvere.
11 Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa;
12 tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje. (Sheol )
13 Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
14 Bwera, chita nafe maere, ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
15 Mwana wanga, usayende nawo pamodzi, usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
16 Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi.
17 Nʼkopanda phindu kutchera msampha mbalame zikuona!
18 Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe; amangodzitchera okha msampha!
19 Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake.
20 Nzeru ikufuwula mu msewu, ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
21 ikufuwula pa mphambano ya misewu, ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,
22 “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
23 Tamverani mawu anga a chidzudzulo. Ine ndikukuwuzani maganizo anga ndi kukudziwitsani mawu anga.
24 Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera. Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
25 Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale.
26 Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto; ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
27 Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe, tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu, mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
28 “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
29 Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
30 popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
31 Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
32 Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo, ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
33 Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata; adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”