< Miyambo 9 >
1 Nzeru inamanga nyumba yake; inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
2 Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake; inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
3 Nzeruyo inatuma adzakazi ake, kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
4 “Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!” Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
5 “Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
6 Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo; yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”
7 Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo; aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
8 Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
9 Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru; ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.
10 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
11 Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
12 Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa; ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.
13 Uchitsiru ndi mkazi waphokoso, wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
14 Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake, pamalo aatali a mu mzinda,
15 kuti aziyitana anthu ongodutsa, amene akunka nayenda njira zawo.
16 Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17 “Madzi akuba ndiye amatsekemera; chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
18 Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya. (Sheol )