< Miyambo 7 >

1 Mwana wanga, mvera mawu anga; usunge bwino malamulo angawa.
My son, keep my words. Lay up my commandments within you.
2 Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
Keep my commandments and live. Guard my teaching as the apple of your eye.
3 Uchite ngati wawamangirira pa zala zako, ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
Bind them on your fingers. Write them on the tablet of your heart.
4 Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
Tell wisdom, "You are my sister." Call understanding your relative,
5 Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
that they may keep you from the strange woman, from the foreigner who flatters with her words.
6 Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga ndinasuzumira pa zenera.
For at the window of my house, I looked out through my lattice.
7 Ndinaona pakati pa anthu opusa, pakati pa anyamata, mnyamata wina wopanda nzeru.
I saw among the simple ones. I discerned among the youths a young man void of understanding,
8 Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
passing through the street near her corner, he went the way to her house,
9 Inali nthawi yachisisira madzulo, nthawi ya usiku, kuli mdima.
in the twilight, in the evening of the day, in the middle of the night and in the darkness.
10 Ndipo mkaziyo anadzakumana naye, atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
Look, there a woman met him with the attire of a prostitute, and with crafty intent.
11 (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve, iye ndi wosakhazikika pa khomo.
She is loud and defiant. Her feet do not stay in her house.
12 Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika, ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
Now she is in the streets, now in the squares, and lurking at every corner.
13 Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
So she caught him, and kissed him. With an impudent face she said to him:
14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano. Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
"Sacrifices of peace offerings are with me. This day I have paid my vows.
15 Choncho ndinabwera kudzakumana nawe; ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
Therefore I came out to meet you, to diligently seek your face, and I have found you.
16 Pa bedi panga ndayalapo nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
I have spread my couch with carpets of tapestry, with striped cloths of the yarn of Egypt.
17 Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
I have perfumed my bed with myrrh, aloes, and cinnamon.
18 Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa; tiye tisangalatsane mwachikondi!
Come, let's take our fill of loving until the morning. Let's solace ourselves with loving.
19 Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako; wapita ulendo wautali:
For my husband isn't at home. He has gone on a long journey.
20 Anatenga thumba la ndalama ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
He has taken a bag of money with him. He will come home at the full moon."
21 Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo; amukopa ndi mawu ake oshashalika.
With persuasive words, she led him astray. With the flattering of her lips, she seduced him.
22 Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo ngati ngʼombe yopita kukaphedwa, monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
He followed her immediately, as an ox goes to the slaughter, as a stag leaping into a trap,
23 mpaka muvi utalasa chiwindi chake, chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe, osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
till an arrow strikes through his liver, as a bird hurries to the snare, and doesn't know that it will cost his life.
24 Tsono ana inu, ndimvereni; mvetsetsani zimene ndikunena.
Now therefore, son, listen to me. Pay attention to the words of my mouth.
25 Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu; musasochere potsata njira zake.
Do not let your heart turn to her ways. Do not go astray in her paths,
26 Paja iye anagwetsa anthu ambiri; wapha gulu lalikulu la anthu.
for she has thrown down many wounded. Yes, all her slain are a mighty army.
27 Nyumba yake ndi njira yopita ku manda, yotsikira ku malo a anthu akufa. (Sheol h7585)
Her house is the way to Sheol, going down to the chambers of death. (Sheol h7585)

< Miyambo 7 >