< Miyambo 4 >

1 Ananu, mverani malangizo a abambo anu; tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.
שִׁמְעוּ בָנִים מוּסַר אָב וְהַקְשִׁיבוּ לָדַעַת בִּינָֽה׃
2 Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino. Choncho musasiye malangizo anga.
כִּי לֶקַח טוֹב נָתַתִּי לָכֶם תּוֹרָתִי אַֽל־תַּעֲזֹֽבוּ׃
3 Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga; mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.
כִּֽי־בֵן הָיִיתִי לְאָבִי רַךְ וְיָחִיד לִפְנֵי אִמִּֽי׃
4 Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti, “Ugwiritse mawu anga pa mtima pako, usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.
וַיֹּרֵנִי וַיֹּאמֶר לִי יִֽתְמׇךְ־דְּבָרַי לִבֶּךָ שְׁמֹר מִצְוֺתַי וֶחְיֵֽה׃
5 Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu; usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.
קְנֵה חׇכְמָה קְנֵה בִינָה אַל־תִּשְׁכַּח וְאַל־תֵּט מֵאִמְרֵי־פִֽי׃
6 Usasiye nzeru ndipo idzakusunga. Uziyikonda ndipo idzakuteteza.
אַל־תַּעַזְבֶהָ וְתִשְׁמְרֶךָּ אֱהָבֶהָ וְתִצְּרֶֽךָּ׃
7 Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.
רֵאשִׁית חׇכְמָה קְנֵה חׇכְמָה וּבְכׇל־קִנְיָנְךָ קְנֵה בִינָֽה׃
8 Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza; ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.
סַלְסְלֶהָ וּֽתְרוֹמְמֶךָּ תְּכַבֵּדְךָ כִּי תְחַבְּקֶֽנָּה׃
9 Idzayika sangamutu yokongola yamaluwa pamutu pako; idzakupatsa chipewa chaufumu chaulemu.”
תִּתֵּן לְרֹאשְׁךָ לִוְיַת־חֵן עֲטֶרֶת תִּפְאֶרֶת תְּמַגְּנֶֽךָּ׃
10 Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena, ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.
שְׁמַע בְּנִי וְקַח אֲמָרָי וְיִרְבּוּ לְךָ שְׁנוֹת חַיִּֽים׃
11 Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.
בְּדֶרֶךְ חׇכְמָה הֹרֵיתִיךָ הִדְרַכְתִּיךָ בְּמַעְגְּלֵי־יֹֽשֶׁר׃
12 Pamene ukuyenda, mapazi ako sadzawombana; ukamadzathamanga, sudzapunthwa.
בְּֽלֶכְתְּךָ לֹא־יֵצַר צַעֲדֶךָ וְאִם־תָּרוּץ לֹא תִכָּשֵֽׁל׃
13 Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi. Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.
הַחֲזֵק בַּמּוּסָר אַל־תֶּרֶף נִצְּרֶהָ כִּי־הִיא חַיֶּֽיךָ׃
14 Usayende mʼnjira za anthu oyipa kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
בְּאֹרַח רְשָׁעִים אַל־תָּבֹא וְאַל־תְּאַשֵּׁר בְּדֶרֶךְ רָעִֽים׃
15 Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo; uzilambalala nʼkumangopita.
פְּרָעֵהוּ אַל־תַּעֲבׇר־בּוֹ שְׂטֵה מֵעָלָיו וַעֲבֹֽר׃
16 Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa; tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.
כִּי לֹא יִֽשְׁנוּ אִם־לֹא יָרֵעוּ וְֽנִגְזְלָה שְׁנָתָם אִם־לֹא (יכשולו) [יַכְשִֽׁילוּ]׃
17 Paja chakudya chawo ndicho kuchita zoyipa basi ndipo chakumwa chawo ndi chiwawa.
כִּי לָחֲמוּ לֶחֶם רֶשַׁע וְיֵין חֲמָסִים יִשְׁתּֽוּ׃
18 Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.
וְאֹרַח צַדִּיקִים כְּאוֹר נֹגַהּ הוֹלֵךְ וָאוֹר עַד־נְכוֹן הַיּֽוֹם׃
19 Koma njira ya anthu oyipa ili ngati mdima wandiweyani; iwo sadziwa chomwe chimawapunthwitsa.
דֶּרֶךְ רְשָׁעִים כָּאֲפֵלָה לֹא יָדְעוּ בַּמֶּה יִכָּשֵֽׁלוּ׃
20 Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena; tchera khutu ku mawu anga.
בְּנִי לִדְבָרַי הַקְשִׁיבָה לַאֲמָרַי הַט־אׇזְנֶֽךָ׃
21 Usayiwale malangizo angawa, koma uwasunge mu mtima mwako.
אַל־יַלִּיזוּ מֵעֵינֶיךָ שׇׁמְרֵם בְּתוֹךְ לְבָבֶֽךָ׃
22 Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza ndipo amachiritsa thupi lake lonse.
כִּֽי־חַיִּים הֵם לְמֹצְאֵיהֶם וּֽלְכׇל־בְּשָׂרוֹ מַרְפֵּֽא׃
23 Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.
מִֽכׇּל־מִשְׁמָר נְצֹר לִבֶּךָ כִּֽי־מִמֶּנּוּ תּוֹצְאוֹת חַיִּֽים׃
24 Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota; ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.
הָסֵר מִמְּךָ עִקְּשׁוּת פֶּה וּלְזוּת שְׂפָתַיִם הַרְחֵק מִמֶּֽךָּ׃
25 Maso ako ayangʼane patsogolo; uziyangʼana kutsogolo molunjika.
עֵינֶיךָ לְנֹכַח יַבִּיטוּ וְעַפְעַפֶּיךָ יַיְשִׁרוּ נֶגְדֶּֽךָ׃
26 Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.
פַּלֵּס מַעְגַּל רַגְלֶךָ וְֽכׇל־דְּרָכֶיךָ יִכֹּֽנוּ׃
27 Usapatukire kumanja kapena kumanzere; usapite kumene kuli zoyipa.
אַֽל־תֵּט־יָמִין וּשְׂמֹאול הָסֵר רַגְלְךָ מֵרָֽע׃

< Miyambo 4 >