< Miyambo 31 >
1 Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:
利慕伊勒王的言语,是他母亲教训他的真言。
2 Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga? Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?
我的儿啊,我腹中生的儿啊, 我许愿得的儿啊!我当怎样教训你呢?
3 Usapereke mphamvu yako kwa akazi. Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.
不要将你的精力给妇女; 也不要有败坏君王的行为。
4 Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu, mafumu sayenera kumwa vinyo. Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa
利慕伊勒啊,君王喝酒,君王喝酒不相宜; 王子说浓酒在那里也不相宜;
5 kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko, nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.
恐怕喝了就忘记律例, 颠倒一切困苦人的是非。
6 Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa, vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;
可以把浓酒给将亡的人喝, 把清酒给苦心的人喝,
7 amwe kuti ayiwale umphawi wawo asakumbukirenso kuvutika kwawo.
让他喝了,就忘记他的贫穷, 不再记念他的苦楚。
8 Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.
你当为哑巴开口, 为一切孤独的伸冤。
9 Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.
你当开口按公义判断, 为困苦和穷乏的辨屈。
10 Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
才德的妇人谁能得着呢? 她的价值远胜过珍珠。
11 Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira ndipo mwamunayo sasowa phindu.
她丈夫心里倚靠她, 必不缺少利益;
12 Masiku onse a moyo wake mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.
她一生使丈夫有益无损。
13 Iye amafunafuna ubweya ndi thonje; amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
她寻找羊绒和麻, 甘心用手做工。
14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda, amakatenga chakudya chake kutali.
她好像商船从远方运粮来,
15 Iye amadzuka kusanache kwenikweni; ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.
未到黎明她就起来, 把食物分给家中的人, 将当做的工分派婢女。
16 Iye amalingalira za munda ndi kuwugula; ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.
她想得田地就买来; 用手所得之利栽种葡萄园。
17 Iye amavala zilimbe nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.
她以能力束腰, 使膀臂有力。
18 Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse.
她觉得所经营的有利; 她的灯终夜不灭。
19 Iye amadzilukira thonje ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.
她手拿捻线竿, 手把纺线车。
20 Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
她张手周济困苦人, 伸手帮补穷乏人。
21 Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu; pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.
她不因下雪为家里的人担心, 因为全家都穿着朱红衣服。
22 Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake; amavala zovala zabafuta ndi zapepo.
她为自己制作绣花毯子; 她的衣服是细麻和紫色布做的。
23 Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda, ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.
她丈夫在城门口与本地的长老同坐, 为众人所认识。
24 Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa; amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
她做细麻布衣裳出卖, 又将腰带卖与商家。
25 Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake; ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
能力和威仪是她的衣服; 她想到日后的景况就喜笑。
26 Iye amayankhula mwanzeru, amaphunzitsa anthu mwachikondi.
她开口就发智慧; 她舌上有仁慈的法则。
27 Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.
她观察家务, 并不吃闲饭。
28 Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala; ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
她的儿女起来称她有福; 她的丈夫也称赞她,
29 “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana koma iwe umawaposa onsewa.”
说:才德的女子很多, 惟独你超过一切。
30 Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa; koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
艳丽是虚假的,美容是虚浮的; 惟敬畏耶和华的妇女必得称赞。
31 Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.
愿她享受操作所得的; 愿她的工作在城门口荣耀她。