< Miyambo 29 >

1 Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri, adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.
איש תוכחות מקשה-ערף-- פתע ישבר ואין מרפא
2 Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa, koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.
ברבות צדיקים ישמח העם ובמשל רשע יאנח עם
3 Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake, koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.
איש-אהב חכמה ישמח אביו ורעה זונות יאבד-הון
4 Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo, koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.
מלך--במשפט יעמיד ארץ ואיש תרומות יהרסנה
5 Munthu woshashalika mnzake, akudziyalira ukonde mapazi ake.
גבר מחליק על-רעהו רשת פורש על-פעמיו
6 Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake, koma wochita chilungamo amayimba lokoma.
בפשע איש רע מוקש וצדיק ירון ושמח
7 Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.
ידע צדיק דין דלים רשע לא-יבין דעת
8 Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda, koma anthu anzeru amaletsa ukali.
אנשי לצון יפיחו קריה וחכמים ישיבו אף
9 Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.
איש-חכם--נשפט את-איש אויל ורגז ושחק ואין נחת
10 Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro koma anthu olungama amasamalira moyo wake.
אנשי דמים ישנאו-תם וישרים יבקשו נפשו
11 Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.
כל-רוחו יוציא כסיל וחכם באחור ישבחנה
12 Ngati wolamulira amvera zabodza, akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.
משל מקשיב על-דבר-שקר-- כל-משרתיו רשעים
13 Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti: Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.
רש ואיש תככים נפגשו-- מאיר עיני שניהם יהוה
14 Ngati mfumu iweruza osauka moyenera, mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.
מלך שופט באמת דלים-- כסאו לעד יכון
15 Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.
שבט ותוכחת יתן חכמה ונער משלח מביש אמו
16 Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka, koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.
ברבות רשעים ירבה-פשע וצדיקים במפלתם יראו
17 Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.
יסר בנך ויניחך ויתן מעדנים לנפשך
18 Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo; koma wodala ndi amene amasunga malamulo.
באין חזון יפרע עם ושמר תורה אשרהו
19 Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi; ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.
בדברים לא-יוסר עבד כי-יבין ואין מענה
20 Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.
חזית--איש אץ בדבריו תקוה לכסיל ממנו
21 Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana, potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.
מפנק מנער עבדו ואחריתו יהיה מנון
22 Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano, ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.
איש-אף יגרה מדון ובעל חמה רב-פשע
23 Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
גאות אדם תשפילנו ושפל-רוח יתמך כבוד
24 Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe; amalumbira koma osawulula kanthu.
חולק עם-גנב שונא נפשו אלה ישמע ולא יגיד
25 Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha, koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.
חרדת אדם יתן מוקש ובוטח ביהוה ישגב
26 Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima, koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.
רבים מבקשים פני-מושל ומיהוה משפט-איש
27 Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo; koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.
תועבת צדיקים איש עול ותועבת רשע ישר-דרך

< Miyambo 29 >