< Miyambo 28 >

1 Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa, koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.
Huye el impío sin que nadie le persiga: mas el justo está confiado como un leoncillo.
2 Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri, koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.
Por la rebelión de la tierra sus príncipes son muchos: mas por el hombre entendido y sabio permanecerá sin mutación.
3 Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.
El hombre pobre, y robador de los pobres es lluvia de avenida, y sin pan.
4 Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa, koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.
Los que dejan la ley, alaban al impío: mas los que la guardan, contenderán con ellos.
5 Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama, koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.
Los hombres malos no entienden el juicio: mas los que buscan a Jehová, entienden todas las cosas.
6 Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.
Mejor es el pobre que camina en su perfección, que el de perversos caminos, y rico.
7 Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu, koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.
El que guarda la ley, es hijo prudente: mas el que es compañero de glotones, avergüenza a su padre.
8 Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.
El que aumenta sus riquezas con usura y recambio, para que se dé a los pobres lo allega.
9 Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.
El que aparta su oído por no oír la ley, su oración también será abominable.
10 Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa adzagwera mu msampha wake womwe, koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.
El que hace errar a los rectos por el mal camino, él caerá en su misma sima: mas los perfectos heredarán el bien.
11 Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.
El hombre rico es sabio en su opinión: mas el pobre entendido le examinará.
12 Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu; koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.
Cuando los justos se alegran, grande es la gloria; y cuando los impíos son levantados, el hombre será buscado.
13 Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
El que encubre sus pecados, nunca prosperará: mas el que confiesa, y se aparta, alcanzará misericordia.
14 Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse, koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.
Bienaventurado el hombre que siempre teme: mas el que endurece su corazón, caerá en mal.
15 Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.
León bramador, y oso hambriento es el príncipe impío sobre el pueblo pobre.
16 Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.
El príncipe falto de entendimiento multiplica los agravios: mas el que aborrece la avaricia, alargará los días.
17 Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize.
El hombre que hace violencia con sangre de persona, hasta el sepulcro huirá; y nadie le sustentará.
18 Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.
El que camina en integridad, será salvo: mas el de perversos caminos, caerá en alguno.
19 Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.
El que labra su tierra se hartará de pan: mas el que sigue a los ociosos, se hartará de pobreza.
20 Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.
El hombre de verdad tendrá muchas bendiciones: mas el que se apresura a enriquecer, no será sin culpa.
21 Kukondera si kwabwino, ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.
Tener respeto a personas en el juicio, no es bueno: aun por un bocado de pan prevaricará el hombre.
22 Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.
Apresúrase a ser rico el hombre de mal ojo, y no conoce que le ha de venir pobreza.
23 Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.
El que reprende al hombre que vuelve atrás, hallará gracia, más que el que lisonjea con la lengua.
24 Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.
El que roba a su padre y a su madre, y dice que no es maldad, compañero es del hombre destruidor.
25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano, koma amene amadalira Yehova adzalemera.
El altivo de ánimo revuelve contiendas: mas el que confía en Jehová, engordará.
26 Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.
El que confía en su corazón es insensato: mas el que camina en sabiduría, él escapará.
27 Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.
El que da al pobre, nunca tendrá pobreza: mas el que del pobre aparta sus ojos, tendrá muchas maldiciones.
28 Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala, koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.
Cuando los impíos son levantados, el hombre cuerdo se esconderá: mas cuando perecen, los justos se multiplican.

< Miyambo 28 >