< Miyambo 27 >

1 Usamanyadire za mawa, pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.
Do not boast about tomorrow; for you do not know what a day may bring forth.
2 Munthu wina akutamande, koma osati wekha; mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.
Let another man praise you, and not your own mouth; a stranger, and not your own lips.
3 Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri, koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.
A stone is heavy, and sand is a burden; but a fool's provocation is heavier than both.
4 Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa. Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.
Wrath is cruel, and anger is overwhelming; but who is able to stand before jealousy?
5 Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino kuposa chikondi chobisika.
Better is open rebuke than hidden love.
6 Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino, koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.
Faithful are the wounds of a friend; although the kisses of an enemy are profuse.
7 Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.
A full soul loathes a honeycomb; but to a hungry soul, every bitter thing is sweet.
8 Munthu amene wasochera ku nyumba kwake, ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.
As a bird that wanders from her nest, so is a man who wanders from his home.
9 Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
Perfume and incense bring joy to the heart; so does earnest counsel from a man's friend.
10 Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako, ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto; mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
Do not forsake your friend and your father's friend. Do not go to your brother's house in the day of your disaster: better is a neighbor who is near than a distant brother.
11 Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga; pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.
Be wise, my son, and bring joy to my heart, then I can answer my tormentor.
12 Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.
A prudent man sees danger and takes refuge; but the simple pass on, and suffer for it.
13 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.
Take his garment when he puts up collateral for a stranger. Hold it for a wayward woman.
14 Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri, anthu adzamuyesa kuti akutemberera.
He who blesses his neighbor with a loud voice early in the morning, it will be taken as a curse by him.
15 Mkazi wolongolola ali ngati mvula yamvumbi.
A continual dropping on a rainy day and a contentious wife are alike:
16 Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.
restraining her is like restraining the wind, or like grasping oil in his right hand.
17 Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake, chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.
Iron sharpens iron; so a man sharpens his friend's countenance.
18 Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake, ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.
Whoever tends the fig tree shall eat its fruit. He who looks after his master shall be honored.
19 Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi, chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.
As water reflects a face, so a man's heart reflects the man.
20 Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta. (Sheol h7585)
Sheol and Abaddon are never satisfied; and a man's eyes are never satisfied. (Sheol h7585)
21 Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo, chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.
The crucible is for silver, and the furnace for gold; but man is refined by his praise.
22 Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo ndi musi ngati chimanga, uchitsiru wakewo sudzachoka.
Though you grind a fool in a mortar with a pestle along with grain, yet his foolishness will not be removed from him.
23 Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili. Kodi usamalire bwino ziweto zako?
Know well the state of your flocks, and pay attention to your herds:
24 Paja chuma sichikhala mpaka muyaya, ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.
for riches are not forever, nor does even the crown endure to all generations.
25 Pamene udzu watha, msipu nʼkumera; ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,
The hay is removed, and the new growth appears, the grasses of the hills are gathered in.
26 ana ankhosa adzakupatsani chovala ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.
The lambs are for your clothing, and the goats are the price of a field.
27 Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri kuti muzidya inuyo ndi banja lanu ndi kudyetsa antchito anu aakazi.
There will be plenty of goats' milk for your food, for your family's food, and for the nourishment of your servant girls.

< Miyambo 27 >