< Miyambo 26 >
1 Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola, ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.
Som snø um sumaren og regn i skurden, so høver ikkje æra for ein dåre.
2 Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira, ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.
Som sporven flaksar burt og svala flyg, so råkar ikkje grunnlaus forbanning.
3 Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu, choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.
Svipa til hesten, taum til asnet, og ris til ryggen på dårar.
4 Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake, kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.
Svar ikkje dåren etter hans dårskap, so du ei skal verta lik han, du og!
5 Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake, kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.
Svara dåren etter hans dårskap, so han ei skal tykkja han sjølv er vis!
6 Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.
Føterne høgg han av seg, og vald fær han drikka, han som sender bod med ein dåre.
7 Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
Visne heng vanfør manns føter, so og ordtak i munnen på dårar
8 Kupereka ulemu kwa chitsiru zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.
som å binda ein stein i slyngja, soleis er det å gjeva ein dåre æra.
9 Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
Som klungergrein i handi på drukken mann, so er ordtak i munnen på dårar.
10 Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda, ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.
Som ein skyttar som sårar alle, so er den som leiger dåren og kvar som fer framum.
11 Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.
Som hund som snur seg til si eigi spya, so er ein dåre som kjem att til narreskapen sin.
12 Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.
Ser du ein mann som tykkjer sjølv at han er vis, då er det større von for dåren enn for honom.
13 Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango, mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”
Letingen segjer: «D’er villdyr på vegen, ei løva i gatorne.»
14 Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake, momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.
Døri snur seg på gjengi, og letingen snur seg i sengi.
15 Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale; zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.
Stikk den late si hand i fatet, han evast med å ta ho upp til munnen att.
16 Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.
Letingen tykkjest visare vera enn sju som gjev vituge svar.
17 Munthu wongolowera mikangano imene si yake ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.
Han triv i øyro på framumfarande hund, han som ryk upp i sinne for trætta som ikkje kjem han ved.
18 Monga munthu wamisala amene akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
Som ein galen som skyt med brennende pilar - drepande skot -
19 ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake, amene amati, “Ndimangoseka chabe!”
so er ein mann som svik sin næste og segjer: «Eg gjorde det berre på gaman.»
20 Pakasowa nkhuni, moto umazima; chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.
Når veden tryt, so sloknar elden, er baktalar burte, stoggar striden.
21 Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto, ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.
Som kol vert til gløder og ved til eld, so kveikjer kranglaren kiv.
22 Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma; chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.
Baktalar-ord er som lostemat, dei glid so godt ned i livet.
23 Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.
Som sylv-glasering på skålbrot er brennande lippor når hjarta er vondt.
24 Munthu wachidani amayankhula zabwino pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
Med lipporne skaper ein uven seg til, men inni seg gøymer han svik.
25 Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire, pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
Gjer han seg blidmælt, tru honom ei, for sju slag styggedom bur i hans hjarta.
26 Ngakhale amabisa chidani mochenjera, koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.
Hatet dyl seg i svik, men lyt syna sin vondskap i folkemugen.
27 Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha; ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.
Den som grev ei grav, skal stupa nedi, den som velter ein stein, skal få han yver seg att.
28 Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka, ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.
Den falske tunga hatar deim som ho hev krasa, og den sleipe munnen fører til fall.