< Miyambo 25 >
1 Iyi ndi miyambo inanso ya Solomoni, imene anthu a Hezekiya mfumu ya ku Yuda analemba.
2 Ulemerero wa Mulungu uli pa kubisa zinthu; ulemerero wa mafumu uli pa kufufuza zinthuzo.
3 Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi, ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.
4 Chotsa zoyipa mʼsiliva ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.
5 Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu; ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.
6 Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu, ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;
7 paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,” kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa. Chimene wachiona ndi maso ako,
8 usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu nanga udzachita chiyani pa mapeto pake ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?
9 Kamba mlandu ndi mnansi wako, koma osawulula chinsinsi cha munthu wina
10 kuopa kuti wina akamva mawu ako adzakuchititsa manyazi ndipo mbiri yako yoyipa sidzatha.
11 Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.
12 Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.
13 Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola kwa anthu amene amutuma; iye amaziziritsa mtima bwana wake.
14 Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.
15 Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu, ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.
16 Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira, kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.
17 Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako ukawirikiza kupita, udzadana naye.
18 Munthu wochitira mnzake umboni wonama, ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
19 Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto, kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.
20 Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira kapena kuthira mchere pa chilonda.
21 Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.
22 Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake, ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.
23 Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula, chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.
24 Nʼkwabwino kukhala pa ngodya ya denga kuposa kukhala mʼnyumba ndi mkazi wolongolola.
25 Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.
26 Munthu wolungama amene amagonjera munthu woyipa ali ngati kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oyipa.
27 Sibwino kudya uchi wambiri, sibwinonso kudzifunira wekha ulemu.
28 Munthu amene samatha kudziretsa ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.