< Miyambo 24 >
1 Usachitire nsanje anthu oyipa, usalakalake kuti uzikhala nawo,
2 pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa, ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.
3 Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
4 Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.
5 Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri, ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
6 Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo. Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.
7 Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru; chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.
8 Amene amakonzekera kuchita zoyipa adzatchedwa mvundulamadzi.
9 Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo, ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.
10 Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti mphamvu yako ndi yochepadi!
11 Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe; uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
12 Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?
13 Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino; uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
14 Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako; ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo, ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.
15 Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa. Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
16 paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso. Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.
17 Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako. Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
18 Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo, angaleke kukwiyira mdaniyo.
19 Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
20 paja munthu woyipa alibe tsogolo. Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.
21 Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu, ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
22 awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi. Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?
23 Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa: Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
24 Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,” anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
25 Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.
26 Woyankhula mawu owona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
27 Ugwiriretu ntchito zako zonse, makamaka za ku munda ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
28 Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
29 Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine; ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”
30 Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31 Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga, mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
32 Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga ndipo ndinatolapo phunziro ili:
33 Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,” kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
34 umphawi udzafika pa iwe ngati mbala ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.