< Miyambo 23 >
1 Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira, uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,
CUANDO te sentares á comer con algún señor, considera bien lo que estuviere delante de ti;
2 ngati ndiwe munthu wadyera udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.
Y pon cuchillo á tu garganta, si tienes gran apetito.
3 Usasirire zakudya zake, pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.
No codicies sus manjares delicados, porque es pan engañoso.
4 Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.
No trabajes por ser rico; pon coto á tu prudencia.
5 Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo. Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.
¿Has de poner tus ojos en las riquezas, siendo ningunas? porque hacerse han alas, como alas de águila, y volarán al cielo.
6 Usadye chakudya cha munthu waumbombo, usalakalake zakudya zake zokoma;
No comas pan de [hombre de] mal ojo, ni codicies sus manjares:
7 paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.
Porque cual es su pensamiento en su alma, tal es él. Come y bebe, te dirá; mas su corazón no está contigo.
8 Udzasanza zimene wadyazo ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.
Vomitarás la parte que tú comiste, y perderás tus suaves palabras.
9 Usayankhule munthu wopusa akumva, pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.
No hables á oídos del necio; porque menospreciará la prudencia de tus razones.
10 Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,
No traspases el término antiguo, ni entres en la heredad de los huérfanos:
11 paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.
Porque el defensor de ellos es el Fuerte, el cual juzgará la causa de ellos contra ti.
12 Mtima wako uzikhala pa malangizo ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.
Aplica tu corazón á la enseñanza, y tus oídos á las palabras de sabiduría.
13 Usaleke kumulangiza mwana; ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.
No rehuses la corrección del muchacho: [porque] si lo hirieres con vara, no morirá.
14 Ukamukwapula ndi tsatsa udzapulumutsa moyo wake. (Sheol )
Tú lo herirás con vara, y librarás su alma del infierno. (Sheol )
15 Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru, inenso mtima wanga udzakondwera.
Hijo mío, si tu corazón fuere sabio, también á mí se me alegrará el corazón;
16 Mtima wanga udzakondwera pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.
Mis entrañas también se alegrarán, cuando tus labios hablaren cosas rectas.
17 Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa, koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.
No tenga tu corazón envidia de los pecadores, antes [persevera] en el temor de Jehová todo tiempo:
18 Ndithu za mʼtsogolo zilipo ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.
Porque ciertamente hay fin, y tu esperanza no será cortada.
19 Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.
Oye tú, hijo mío, y sé sabio, y endereza tu corazón al camino.
20 Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.
No estés con los bebedores de vino, ni con los comedores de carne:
21 Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi ndipo aulesi adzavala sanza.
Porque el bebedor y el comilón empobrecerán: y el sueño hará vestir vestidos rotos.
22 Mvera abambo ako amene anakubala, usanyoze amayi ako pamene akalamba.
Oye á tu padre, á aquel que te engendró; y cuando tu madre envejeciere, no la menosprecies.
23 Gula choonadi ndipo usachigulitse; ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.
Compra la verdad, y no la vendas; la sabiduría, la enseñanza, y la inteligencia.
24 Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu; Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
Mucho se alegrará el padre del justo: y el que engendró sabio se gozará con él.
25 Abambo ndi amayi ako asangalale; amene anakubereka akondwere!
Alégrense tu padre y tu madre, y gócese la que te engendró.
26 Mwana wanga, undikhulupirire ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.
Dame, hijo mío, tu corazón, y miren tus ojos por mis caminos.
27 Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama; ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.
Porque sima profunda es la ramera, y pozo angosto la extraña.
28 Amabisala ngati mbala yachifwamba, ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.
También ella, como robador, acecha, y multiplica entre los hombres los prevaricadores.
29 Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo? Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?
¿Para quién será el ay? ¿para quién el ay? ¿para quién las rencillas? ¿para quién las quejas? ¿para quién las heridas en balde? ¿para quién lo amoratado de los ojos?
30 Ndi amene amakhalitsa pa mowa, amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.
Para los que se detienen mucho en el vino, para los que van buscando la mistura.
31 Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akuwira mʼchikho pamene akumweka bwino!
No mires al vino cuando rojea, cuando resplandece su color en el vaso: éntrase suavemente;
32 Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amajompha ngati mphiri.
[Mas] al fin como serpiente morderá, y como basilisco dará dolor:
33 Maso ako adzaona zinthu zachilendo ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.
Tus ojos mirarán las extrañas, y tu corazón hablará perversidades.
34 Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.
Y serás como el que yace en medio de la mar, ó como el que está en la punta de un mastelero.
35 Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe! Andimenya koma sindinamve kanthu! Kodi ndidzuka nthawi yanji? Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”
[Y dirás]: Hiriéronme, mas no me dolió; azotáronme, mas no lo sentí; cuando despertare, aun lo tornaré á buscar.