< Miyambo 22 >
1 Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri; kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.
2 Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova.
3 Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.
4 Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.
5 Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha, koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.
6 Mwana muzimuphunzitsa njira yake, ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
7 Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.
8 Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto, ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.
9 Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.
10 Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha; mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.
11 Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino, adzakhala bwenzi la mfumu.
12 Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu, koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.
13 Munthu waulesi amati, “Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”
14 Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama; amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.
15 Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana, koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.
16 Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.
17 Utchere khutu lako ndipo umvere mawu anzeru; uyike mtima wako pa zimene ndikukuphunzitsa kuti udziwe.
18 Zidzakhala zokondweretsa ngati uzisunga mu mtima mwako ndi wokonzeka kuziyankhula.
19 Ndakuphunzitsa zimenezi lero koma makamaka uziopa Yehova.
20 Kodi suja ndinakulembera malangizo makumi atatu okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21 malangizo okudziwitsa zolungama ndi zoona ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?
22 Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu,
23 pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.
24 Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya
25 kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake ndi kukodwa mu msampha.
26 Usakhale munthu wopereka chikole kapena kukhala mboni pa ngongole;
27 ngati ulephera kupeza njira yolipirira adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.
28 Usasunthe mwala wamʼmalire akalekale amene anayikidwa ndi makolo ako.
29 Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzatumikira mafumu; sadzatumikira anthu wamba.