< Miyambo 21 >

1 Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova; Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.
פלגי מים לב מלך ביד יהוה על כל אשר יחפץ יטנו׃
2 Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo, koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
כל דרך איש ישר בעיניו ותכן לבות יהוה׃
3 Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
עשה צדקה ומשפט נבחר ליהוה מזבח׃
4 Maso odzikuza ndi mtima wonyada, zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.
רום עינים ורחב לב נר רשעים חטאת׃
5 Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.
מחשבות חרוץ אך למותר וכל אץ אך למחסור׃
6 Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
פעל אוצרות בלשון שקר הבל נדף מבקשי מות׃
7 Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga, pakuti iwo amakana kuchita zolungama.
שד רשעים יגורם כי מאנו לעשות משפט׃
8 Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota, koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.
הפכפך דרך איש וזר וזך ישר פעלו׃
9 Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba, kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
טוב לשבת על פנת גג מאשת מדונים ובית חבר׃
10 Munthu woyipa amalakalaka zoyipa; sachitira chifundo mnansi wake wovutika.
נפש רשע אותה רע לא יחן בעיניו רעהו׃
11 Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru; koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
בענש לץ יחכם פתי ובהשכיל לחכם יקח דעת׃
12 Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova, ndipo Iye adzawononga woyipayo.
משכיל צדיק לבית רשע מסלף רשעים לרע׃
13 Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.
אטם אזנו מזעקת דל גם הוא יקרא ולא יענה׃
14 Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo, ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.
מתן בסתר יכפה אף ושחד בחק חמה עזה׃
15 Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala, koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.
שמחה לצדיק עשות משפט ומחתה לפעלי און׃
16 Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.
אדם תועה מדרך השכל בקהל רפאים ינוח׃
17 Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
איש מחסור אהב שמחה אהב יין ושמן לא יעשיר׃
18 Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.
כפר לצדיק רשע ותחת ישרים בוגד׃
19 Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
טוב שבת בארץ מדבר מאשת מדונים וכעס׃
20 Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma wopusa amachiwononga.
אוצר נחמד ושמן בנוה חכם וכסיל אדם יבלענו׃
21 Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika, amapeza moyo ndi ulemerero.
רדף צדקה וחסד ימצא חיים צדקה וכבוד׃
22 Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.
עיר גברים עלה חכם וירד עז מבטחה׃
23 Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake sapeza mavuto.
שמר פיו ולשונו שמר מצרות נפשו׃
24 Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri.
זד יהיר לץ שמו עושה בעברת זדון׃
25 Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.
תאות עצל תמיתנו כי מאנו ידיו לעשות׃
26 Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri, koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.
כל היום התאוה תאוה וצדיק יתן ולא יחשך׃
27 Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova, nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!
זבח רשעים תועבה אף כי בזמה יביאנו׃
28 Mboni yonama idzawonongeka, koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.
עד כזבים יאבד ואיש שומע לנצח ידבר׃
29 Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima, koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.
העז איש רשע בפניו וישר הוא יכין דרכיו׃
30 Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu, zimene zingapambane Yehova.
אין חכמה ואין תבונה ואין עצה לנגד יהוה׃
31 Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Yehova amene amapambanitsa.
סוס מוכן ליום מלחמה וליהוה התשועה׃

< Miyambo 21 >