< Miyambo 20 >

1 Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola; aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.
לֵ֣ץ הַ֭יַּין הֹמֶ֣ה שֵׁכָ֑ר וְכָל־שֹׁ֥גֶה בּ֝֗וֹ לֹ֣א יֶחְכָּֽם׃
2 Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango; amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.
נַ֣הַם כַּ֭כְּפִיר אֵ֣ימַת מֶ֑לֶךְ מִ֝תְעַבְּר֗וֹ חוֹטֵ֥א נַפְשֽׁוֹ׃
3 Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano, koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.
כָּב֣וֹד לָ֭אִישׁ שֶׁ֣בֶת מֵרִ֑יב וְכָל־אֱ֝וִ֗יל יִתְגַּלָּֽע׃
4 Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera; kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.
מֵ֭חֹרֶף עָצֵ֣ל לֹא־יַחֲרֹ֑שׁ וְשָׁאַ֖ל בַּקָּצִ֣יר וָאָֽיִן׃
5 Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya, munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.
מַ֣יִם עֲ֭מֻקִּים עֵצָ֣ה בְלֶב־אִ֑ישׁ וְאִ֖ישׁ תְּבוּנָ֣ה יִדְלֶֽנָּה׃
6 Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo, koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?
רָב־אָדָ֗ם יִ֭קְרָא אִ֣ישׁ חַסְדּ֑וֹ וְאִ֥ישׁ אֱ֝מוּנִ֗ים מִ֣י יִמְצָֽא׃
7 Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
מִתְהַלֵּ֣ךְ בְּתֻמּ֣וֹ צַדִּ֑יק אַשְׁרֵ֖י בָנָ֣יו אַחֲרָֽיו׃
8 Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo, imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.
מֶ֗לֶךְ יוֹשֵׁ֥ב עַל־כִּסֵּא־דִ֑ין מְזָרֶ֖ה בְעֵינָ֣יו כָּל־רָֽע׃
9 Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga; ndilibe tchimo lililonse?”
מִֽי־יֹ֭אמַר זִכִּ֣יתִי לִבִּ֑י טָ֝הַ֗רְתִּי מֵחַטָּאתִֽי׃
10 Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa.
אֶ֣בֶן וָ֭אֶבֶן אֵיפָ֣ה וְאֵיפָ֑ה תּוֹעֲבַ֥ת יְ֝הוָ֗ה גַּם־שְׁנֵיהֶֽם׃
11 Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake, ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.
גַּ֣ם בְּ֭מַעֲלָלָיו יִתְנַכֶּר־נָ֑עַר אִם־זַ֖ךְ וְאִם־יָשָׁ֣ר פָּעֳלֽוֹ׃
12 Makutu amene amamva ndi maso amene amaona, zonsezi anazilenga ndi Yehova.
אֹ֣זֶן שֹׁ֭מַעַת וְעַ֣יִן רֹאָ֑ה יְ֝הוָ֗ה עָשָׂ֥ה גַם־שְׁנֵיהֶֽם׃
13 Usakonde tulo ungasauke; khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
אַל־תֶּֽאֱהַ֣ב שֵׁ֭נָה פֶּן־תִּוָּרֵ֑שׁ פְּקַ֖ח עֵינֶ֣יךָ שְֽׂבַֽע־לָֽחֶם׃
14 Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.” Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.
רַ֣ע רַ֭ע יֹאמַ֣ר הַקּוֹנֶ֑ה וְאֹזֵ֥ל ל֝֗וֹ אָ֣ז יִתְהַלָּֽל׃
15 Pali golide ndi miyala yamtengowapatali, koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.
יֵ֣שׁ זָ֭הָב וְרָב־פְּנִינִ֑ים וּכְלִ֥י יְ֝קָ֗ר שִׂפְתֵי־דָֽעַת׃
16 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.
לְֽקַח־בִּ֭גְדוֹ כִּי־עָ֣רַב זָ֑ר וּבְעַ֖ד נָכְרִיָּ֣ה חַבְלֵֽהוּ׃
17 Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.
עָרֵ֣ב לָ֭אִישׁ לֶ֣חֶם שָׁ֑קֶר וְ֝אַחַ֗ר יִמָּֽלֵא־פִ֥יהוּ חָצָֽץ׃
18 Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu; ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.
מַ֭חֲשָׁבוֹת בְּעֵצָ֣ה תִכּ֑וֹן וּ֝בְתַחְבֻּל֗וֹת עֲשֵׂ֣ה מִלְחָמָֽה׃
19 Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi. Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.
גּֽוֹלֶה־סּ֭וֹד הוֹלֵ֣ךְ רָכִ֑יל וּלְפֹתֶ֥ה שְׂ֝פָתָ֗יו לֹ֣א תִתְעָרָֽב׃
20 Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake, moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.
מְ֭קַלֵּל אָבִ֣יו וְאִמּ֑וֹ יִֽדְעַ֥ךְ נֵ֝ר֗וֹ בֶּאֱשׁ֥וּן חֹֽשֶׁךְ׃
21 Cholowa chochipeza mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.
נַ֭חֲלָה מְבֹהֶ֣לֶת בָּרִאשֹׁנָ֑ה וְ֝אַחֲרִיתָ֗הּ לֹ֣א תְבֹרָֽךְ׃
22 Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!” Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.
אַל־תֹּאמַ֥ר אֲשַׁלְּמָה־רָ֑ע קַוֵּ֥ה לַֽ֝יהוָ֗ה וְיֹ֣שַֽׁע לָֽךְ׃
23 Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.
תּוֹעֲבַ֣ת יְ֭הוָה אֶ֣בֶן וָאָ֑בֶן וּמֹאזְנֵ֖י מִרְמָ֣ה לֹא־טֽוֹב׃
24 Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova, tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?
מֵיהוָ֥ה מִצְעֲדֵי־גָ֑בֶר וְ֝אָדָ֗ם מַה־יָּבִ֥ין דַּרְכּֽוֹ׃
25 Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,” popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.
מוֹקֵ֣שׁ אָ֭דָם יָ֣לַע קֹ֑דֶשׁ וְאַחַ֖ר נְדָרִ֣ים לְבַקֵּֽר׃
26 Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu anthu oyipa.
מְזָרֶ֣ה רְ֭שָׁעִים מֶ֣לֶךְ חָכָ֑ם וַיָּ֖שֶׁב עֲלֵיהֶ֣ם אוֹפָֽן׃
27 Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova; imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.
נֵ֣ר יְ֭הוָה נִשְׁמַ֣ת אָדָ֑ם חֹ֝פֵ֗שׂ כָּל־חַדְרֵי־בָֽטֶן׃
28 Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu; chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.
חֶ֣סֶד וֶ֭אֱמֶת יִצְּרוּ־מֶ֑לֶךְ וְסָעַ֖ד בַּחֶ֣סֶד כִּסְאֽוֹ׃
29 Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo, imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.
תִּפְאֶ֣רֶת בַּחוּרִ֣ים כֹּחָ֑ם וַהֲדַ֖ר זְקֵנִ֣ים שֵׂיבָֽה׃
30 Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa, ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.
חַבֻּר֣וֹת פֶּ֭צַע תַּמְר֣וּק בְּרָ֑ע וּ֝מַכּ֗וֹת חַדְרֵי־בָֽטֶן׃

< Miyambo 20 >