< Miyambo 2 >

1 Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
בְּ֭נִי אִם־תִּקַּ֣ח אֲמָרָ֑י וּ֝מִצְוֹתַ֗י תִּצְפֹּ֥ן אִתָּֽךְ׃
2 ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
לְהַקְשִׁ֣יב לַֽחָכְמָ֣ה אָזְנֶ֑ךָ תַּטֶּ֥ה לִ֝בְּךָ֗ לַתְּבוּנָֽה׃
3 ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
כִּ֤י אִ֣ם לַבִּינָ֣ה תִקְרָ֑א לַ֝תְּבוּנָ֗ה תִּתֵּ֥ן קוֹלֶֽךָ׃
4 ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
אִם־תְּבַקְשֶׁ֥נָּה כַכָּ֑סֶף וְֽכַמַּטְמוֹנִ֥ים תַּחְפְּשֶֽׂנָּה׃
5 ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
אָ֗ז תָּ֭בִין יִרְאַ֣ת יְהוָ֑ה וְדַ֖עַת אֱלֹהִ֣ים תִּמְצָֽא׃
6 Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
כִּֽי־יְ֭הוָה יִתֵּ֣ן חָכְמָ֑ה מִ֝פִּ֗יו דַּ֣עַת וּתְבוּנָֽה׃
7 Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
יִצְפֹּ֣ן לַ֭יְשָׁרִים תּוּשִׁיָּ֑ה מָ֝גֵ֗ן לְהֹ֣לְכֵי תֹֽם׃
8 pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama. Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.
לִ֭נְצֹר אָרְח֣וֹת מִשְׁפָּ֑ט וְדֶ֖רֶךְ חֲסִידָ֣יו יִשְׁמֹֽר׃
9 Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo, kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
אָ֗ז תָּ֭בִין צֶ֣דֶק וּמִשְׁפָּ֑ט וּ֝מֵישָׁרִ֗ים כָּל־מַעְגַּל־טֽוֹב׃
10 Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako, kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
כִּֽי־תָב֣וֹא חָכְמָ֣ה בְלִבֶּ֑ךָ וְ֝דַ֗עַת לְֽנַפְשְׁךָ֥ יִנְעָֽם׃
11 Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga; kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.
מְ֭זִמָּה תִּשְׁמֹ֥ר עָלֶ֗יךָ תְּבוּנָ֥ה תִנְצְרֶֽכָּה׃
12 Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa, kwa anthu amabodza,
לְ֭הַצִּ֣ילְךָ מִדֶּ֣רֶךְ רָ֑ע מֵ֝אִ֗ישׁ מְדַבֵּ֥ר תַּהְפֻּכֽוֹת׃
13 amene amasiya njira zolungama namayenda mʼnjira zamdima,
הַ֭עֹ֣זְבִים אָרְח֣וֹת יֹ֑שֶׁר לָ֝לֶ֗כֶת בְּדַרְכֵי־חֹֽשֶׁךְ׃
14 amene amakondwera pochita zoyipa namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
הַ֭שְּׂמֵחִים לַעֲשׂ֥וֹת רָ֑ע יָ֝גִ֗ילוּ בְּֽתַהְפֻּכ֥וֹת רָֽע׃
15 Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota, ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.
אֲשֶׁ֣ר אָרְחֹתֵיהֶ֣ם עִקְּשִׁ֑ים וּ֝נְלוֹזִ֗ים בְּמַעְגְּלוֹתָֽם׃
16 Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo; kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,
לְ֭הַצִּ֣ילְךָ מֵאִשָּׁ֣ה זָרָ֑ה מִ֝נָּכְרִיָּ֗ה אֲמָרֶ֥יהָ הֶחֱלִֽיקָה׃
17 amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.
הַ֭עֹזֶבֶת אַלּ֣וּף נְעוּרֶ֑יהָ וְאֶת־בְּרִ֖ית אֱלֹהֶ֣יהָ שָׁכֵֽחָה׃
18 Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa; njira zake zimamufikitsa ku manda.
כִּ֤י שָׁ֣חָה אֶל־מָ֣וֶת בֵּיתָ֑הּ וְאֶל־רְ֝פָאִ֗ים מַעְגְּלֹתֶֽיהָ׃
19 Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera kapena kupezanso njira zamoyo.
כָּל־בָּ֭אֶיהָ לֹ֣א יְשׁוּב֑וּן וְלֹֽא־יַ֝שִּׂ֗יגוּ אָרְח֥וֹת חַיִּֽים׃
20 Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino, uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.
לְמַ֗עַן תֵּ֭לֵךְ בְּדֶ֣רֶךְ טוֹבִ֑ים וְאָרְח֖וֹת צַדִּיקִ֣ים תִּשְׁמֹֽר׃
21 Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;
כִּֽי־יְשָׁרִ֥ים יִשְׁכְּנוּ אָ֑רֶץ וּ֝תְמִימִ֗ים יִוָּ֥תְרוּ בָֽהּ׃
22 Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo, ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.
וּ֭רְשָׁעִים מֵאֶ֣רֶץ יִכָּרֵ֑תוּ וּ֝בוֹגְדִ֗ים יִסְּח֥וּ מִמֶּֽנָּה׃ פ

< Miyambo 2 >