< Miyambo 19 >
1 Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.
Lepszy jest ubogi, który postępuje uczciwie, niż człowiek o przewrotnych wargach, który jest głupcem.
2 Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru; ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.
Nie jest też dobrze, by dusza nie miała wiedzy, a kto jest prędkich nóg, grzeszy.
3 Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta, mtima wake umakwiyira Yehova.
Głupota człowieka wypacza jego drogę, a jego serce zapala się gniewem przeciwko PANU.
4 Chuma chimachulukitsa abwenzi; koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.
Bogactwo przyciąga wielu przyjaciół, ale ubogi zostaje odłączony od przyjaciela.
5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.
Fałszywy świadek nie uniknie kary, a [kto] mówi kłamstwa, nie ujdzie.
6 Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima, ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.
Wielu uprasza o przychylność dostojnika i każdy jest przyjacielem człowieka hojnego.
7 Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo adzamuthawa kupita kutali. Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.
Wszyscy bracia ubogiego nienawidzą go, tym bardziej oddalają się od niego [jego] przyjaciele; ściga ich słowami, ale ich nie ma.
8 Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.
Kto zdobywa rozum, miłuje swoją duszę, a [kto] strzeże roztropności, znajdzie dobro.
9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.
Fałszywy świadek nie uniknie kary, a kto mówi kłamstwa, zginie.
10 Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado, nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!
Głupiemu nie przystoi życie w rozkoszach, tym mniej słudze panować nad książętami.
11 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga; ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
Roztropność człowieka powściąga jego gniew, a jego chwałą [jest] darować wykroczenie.
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.
Gniew króla jest jak ryk lwa, a jego przychylność jak rosa na trawie.
13 Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.
Głupi syn jest utrapieniem dla swego ojca, a kłótliwa żona jest jak nieustanne kapanie z dachu.
14 Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo; koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
Dom i bogactwo [są] dziedzictwem po ojcach, ale roztropna żona jest od PANA.
15 Ulesi umagonetsa tulo tofa nato ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.
Lenistwo pogrąża w twardym śnie, a leniwa dusza będzie cierpieć głód.
16 Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake, koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.
Kto przestrzega przykazania, zachowuje swoją duszę, [ale] kto gardzi swymi drogami, zginie.
17 Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
Kto lituje się nad ubogim, pożycza PANU, a on mu odpłaci za jego dobrodziejstwo.
18 Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.
Karz swego syna, dopóki jest nadzieja, i niech twoja dusza mu nie pobłaża z powodu jego płaczu.
19 Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango; pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.
[Człowiek] wielkiego gniewu poniesie karę, a jeśli [go] uwolnisz, znowu będziesz musiał [to zrobić].
20 Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru.
Posłuchaj rady i przyjmij pouczenie, abyś był mądry u kresu swych dni.
21 Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
Wiele jest zamysłów w sercu człowieka, ale rada PANA się ostoi.
22 Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.
Pragnienie człowieka to jego dobroczynność i lepszy jest ubogi niż kłamca.
23 Kuopa Yehova kumabweretsa moyo; wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.
Bojaźń PANA [prowadzi] do życia, a kto ją ma, spocznie syty i nie nawiedzi go zło.
24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale; koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.
Leniwy kryje swą rękę pod pachę i do ust jej nie podnosi.
25 Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo; dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.
Uderz szydercę, a prosty będzie roztropniejszy; strofuj rozumnego, a pojmie wiedzę.
26 Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake, ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.
Kto trwoni [dobra] ojca i wypędza matkę, ten jest synem, który przynosi wstyd i hańbę.
27 Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.
Synu mój, przestań słuchać pouczeń, które cię odwodzą od słów rozumnych.
28 Mboni yopanda pake imanyoza cholungama, ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.
Nikczemny świadek naśmiewa się z sądu, a usta niegodziwych pożerają nieprawość.
29 Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa, ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.
Sądy są przygotowane dla szyderców, a razy na grzbiet głupców.