< Miyambo 17 >

1 Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere, kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano.
טֹ֤וב פַּ֣ת חֲ֭רֵבָה וְשַׁלְוָה־בָ֑הּ מִ֝בַּ֗יִת מָלֵ֥א זִבְחֵי־רִֽיב׃
2 Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale.
עֶֽבֶד־מַשְׂכִּ֗יל יִ֭מְשֹׁל בְּבֵ֣ן מֵבִ֑ישׁ וּבְתֹ֥וךְ אַ֝חִ֗ים יַחֲלֹ֥ק נַחֲלָֽה׃
3 Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.
מַצְרֵ֣ף לַ֭כֶּסֶף וְכ֣וּר לַזָּהָ֑ב וּבֹחֵ֖ן לִבֹּ֣ות יְהוָֽה׃
4 Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa; munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.
מֵ֭רַע מַקְשִׁ֣יב עַל־שְׂפַת־אָ֑וֶן שֶׁ֥קֶר מֵ֝זִין עַל־לְשֹׁ֥ון הַוֹּֽת׃
5 Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake; amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.
לֹעֵ֣ג לָ֭רָשׁ חֵרֵ֣ף עֹשֵׂ֑הוּ שָׂמֵ֥חַ לְ֝אֵ֗יד לֹ֣א יִנָּקֶֽה׃
6 Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
עֲטֶ֣רֶת זְ֭קֵנִים בְּנֵ֣י בָנִ֑ים וְתִפְאֶ֖רֶת בָּנִ֣ים אֲבֹותָֽם׃
7 Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru, nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu?
לֹא־נָאוָ֣ה לְנָבָ֣ל שְׂפַת־יֶ֑תֶר אַ֝֗ף כִּֽי־לְנָדִ֥יב שְׂפַת־שָֽׁקֶר׃
8 Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo; kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera.
אֶֽבֶן־חֵ֣ן הַ֭שֹּׁחַד בְּעֵינֵ֣י בְעָלָ֑יו אֶֽל־כָּל־אֲשֶׁ֖ר יִפְנֶ֣ה יַשְׂכִּֽיל׃
9 Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi; wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.
מְֽכַסֶּה־פֶּ֭שַׁע מְבַקֵּ֣שׁ אַהֲבָ֑ה וְשֹׁנֶ֥ה בְ֝דָבָ֗ר מַפְרִ֥יד אַלּֽוּף׃
10 Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.
תֵּ֣חַת גְּעָרָ֣ה בְמֵבִ֑ין מֵהַכֹּ֖ות כְּסִ֣יל מֵאָֽה׃
11 Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi; ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza.
אַךְ־מְרִ֥י יְבַקֶּשׁ־רָ֑ע וּמַלְאָ֥ךְ אַ֝כְזָרִ֗י יְשֻׁלַּח־בֹּֽו׃
12 Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.
פָּגֹ֬ושׁ דֹּ֣ב שַׁכּ֣וּל בְּאִ֑ישׁ וְאַל־כְּ֝סִ֗יל בְּאִוַּלְתֹּֽו׃
13 Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino, ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake.
מֵשִׁ֣יב רָ֭עָה תַּ֣חַת טֹובָ֑ה לֹא־תָמִישׁ (תָמ֥וּשׁ) רָ֝עָ֗ה מִבֵּיתֹֽו׃
14 Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi, choncho uzichokapo mkangano usanayambe.
פֹּ֣וטֵֽר מַ֭יִם רֵאשִׁ֣ית מָדֹ֑ון וְלִפְנֵ֥י הִ֝תְגַּלַּ֗ע הָרִ֥יב נְטֹֽושׁ׃
15 Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa, zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.
מַצְדִּ֣יק רָ֭שָׁע וּמַרְשִׁ֣יעַ צַדִּ֑יק תֹּועֲבַ֥ת יְ֝הוָ֗ה גַּם־שְׁנֵיהֶֽם׃
16 Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru poti iyeyo mutu wake sumayenda bwino?
לָמָּה־זֶּ֣ה מְחִ֣יר בְּיַד־כְּסִ֑יל לִקְנֹ֖ות חָכְמָ֣ה וְלֶב־אָֽיִן׃
17 Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse, ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.
בְּכָל־עֵ֭ת אֹהֵ֣ב הָרֵ֑עַ וְאָ֥ח לְ֝צָרָ֗ה יִוָּלֵֽד׃
18 Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.
אָדָ֣ם חֲסַר־לֵ֭ב תֹּוקֵ֣עַ כָּ֑ף עֹרֵ֥ב עֲ֝רֻבָּ֗ה לִפְנֵ֥י רֵעֵֽהוּ׃
19 Wokonda zolakwa amakonda mkangano, ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko.
אֹ֣הֵֽב פֶּ֭שַׁע אֹהֵ֣ב מַצָּ֑ה מַגְבִּ֥יהַּ פִּ֝תְחֹ֗ו מְבַקֶּשׁ־שָֽׁבֶר׃
20 Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino; ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto.
עִקֶּשׁ־לֵ֭ב לֹ֣א יִמְצָא־טֹ֑וב וְנֶהְפָּ֥ךְ בִּ֝לְשֹׁונֹ֗ו יִפֹּ֥ול בְּרָעָֽה׃
21 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake, abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe.
יֹלֵ֣ד כְּ֭סִיל לְת֣וּגָה לֹ֑ו וְלֹֽא־יִ֝שְׂמַ֗ח אֲבִ֣י נָבָֽל׃
22 Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino, koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.
לֵ֣ב שָׂ֭מֵחַ יֵיטִ֣ב גֵּהָ֑ה וְר֥וּחַ נְ֝כֵאָ֗ה תְּיַבֶּשׁ־גָּֽרֶם׃
23 Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri kuti apotoze chiweruzo cholungama.
שֹׁ֣חַד מֵ֭חֵיק רָשָׁ֣ע יִקָּ֑ח לְ֝הַטֹּ֗ות אָרְחֹ֥ות מִשְׁפָּֽט׃
24 Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru, koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi.
אֶת־פְּנֵ֣י מֵבִ֣ין חָכְמָ֑ה וְעֵינֵ֥י כְ֝סִ֗יל בִּקְצֵה־אָֽרֶץ׃
25 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.
כַּ֣עַס לְ֭אָבִיו בֵּ֣ן כְּסִ֑יל וּ֝מֶ֗מֶר לְיֹולַדְתֹּֽו׃
26 Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa, kapena kulanga anthu osalakwa.
גַּ֤ם עֲנֹ֣ושׁ לַצַּדִּ֣יק לֹא־טֹ֑וב לְהַכֹּ֖ות נְדִיבִ֣ים עַל־יֹֽשֶׁר׃
27 Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu, ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu.
חֹושֵׂ֣ךְ אֲ֭מָרָיו יֹודֵ֣עַ דָּ֑עַת וְקַר־ (יְקַר)־ר֝֗וּחַ אִ֣ישׁ תְּבוּנָֽה׃
28 Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete; ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
גַּ֤ם אֱוִ֣יל מַ֭חֲרִישׁ חָכָ֣ם יֵחָשֵׁ֑ב אֹטֵ֖ם שְׂפָתָ֣יו נָבֹֽון׃

< Miyambo 17 >