< Miyambo 15 >

1 Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.
מענה-רך ישיב חמה ודבר-עצב יעלה-אף
2 Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.
לשון חכמים תיטיב דעת ופי כסילים יביע אולת
3 Maso a Yehova ali ponseponse, amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.
בכל-מקום עיני יהוה צפות רעים וטובים
4 Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo, koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.
מרפא לשון עץ חיים וסלף בה שבר ברוח
5 Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake, koma wochenjera amasamala chidzudzulo.
אויל--ינאץ מוסר אביו ושמר תוכחת יערים
6 Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.
בית צדיק חסן רב ובתבואת רשע נעכרת
7 Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru; koma mitima ya zitsiru sitero.
שפתי חכמים יזרו דעת ולב כסילים לא-כן
8 Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.
זבח רשעים תועבת יהוה ותפלת ישרים רצונו
9 Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.
תועבת יהוה דרך רשע ומרדף צדקה יאהב
10 Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Odana ndi chidzudzulo adzafa.
מוסר רע לעזב ארח שונא תוכחת ימות
11 Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova, nanji mitima ya anthu! (Sheol h7585)
שאול ואבדון נגד יהוה אף כי-לבות בני-אדם (Sheol h7585)
12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa; iye sapita kwa anthu anzeru.
לא יאהב-לץ הוכח לו אל-חכמים לא ילך
13 Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe, koma mtima wosweka umawawitsa moyo.
לב שמח ייטב פנים ובעצבת-לב רוח נכאה
14 Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.
לב נבון יבקש-דעת ופני (ופי) כסילים ירעה אולת
15 Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.
כל-ימי עני רעים וטוב-לב משתה תמיד
16 Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova, kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.
טוב-מעט ביראת יהוה-- מאוצר רב ומהומה בו
17 Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi, kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.
טוב ארחת ירק ואהבה-שם-- משור אבוס ושנאה-בו
18 Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano, koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.
איש חמה יגרה מדון וארך אפים ישקיט ריב
19 Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga, koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.
דרך עצל כמשכת חדק וארח ישרים סללה
20 Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.
בן חכם ישמח-אב וכסיל אדם בוזה אמו
21 Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.
אולת שמחה לחסר-לב ואיש תבונה יישר-לכת
22 Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.
הפר מחשבות באין סוד וברב יועצים תקום
23 Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera, ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.
שמחה לאיש במענה-פיו ודבר בעתו מה-טוב
24 Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo kuti apewe malo okhala anthu akufa. (Sheol h7585)
ארח חיים למעלה למשכיל-- למען סור משאול מטה (Sheol h7585)
25 Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.
בית גאים יסח יהוה ויצב גבול אלמנה
26 Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova, koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.
תועבת יהוה מחשבות רע וטהרים אמרי-נעם
27 Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.
עכר ביתו בוצע בצע ושונא מתנת יחיה
28 Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.
לב צדיק יהגה לענות ופי רשעים יביע רעות
29 Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.
רחוק יהוה מרשעים ותפלת צדיקים ישמע
30 Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.
מאור-עינים ישמח-לב שמועה טובה תדשן-עצם
31 Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo adzakhala pakati pa anthu anzeru.
אזן--שמעת תוכחת חיים בקרב חכמים תלין
32 Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha, koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.
פורע מוסר מואס נפשו ושומע תוכחת קונה לב
33 Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru, ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.
יראת יהוה מוסר חכמה ולפני כבוד ענוה

< Miyambo 15 >