< Miyambo 14 >
1 Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.
2 Amene amayenda molungama amaopa Yehova, koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.
3 Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana, koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.
4 Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya, koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.
5 Mboni yokhulupirika sinama, koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.
6 Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza, koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga.
7 Khala kutali ndi munthu wopusa chifukwa sudzapeza mawu a nzeru.
8 Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake. Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.
9 Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo, koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.
10 Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake, ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.
11 Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka, koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.
12 Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.
13 Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa, ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni.
14 Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake, koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake.
15 Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.
16 Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa, koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.
17 Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru, ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.
18 Anthu opusa amalandira uchitsiru, koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.
19 Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino, ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.
20 Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda, koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.
21 Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.
22 Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.
23 Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu, koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.
24 Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe, koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.
25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo, koma mboni yabodza imaphetsa.
26 Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.
27 Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo, kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.
28 Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu, koma popanda anthu kalonga amawonongeka.
29 Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.
30 Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imawoletsa mafupa.
31 Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.
32 Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe, koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo.
33 Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu, koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.
34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
35 Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru, koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.