< Miyambo 12 >
1 Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu, koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.
Chi ama la disciplina ama la scienza, chi odia la correzione è stolto.
2 Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova, koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.
Il buono si attira il favore del Signore, ma egli condanna l'intrigante.
3 Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa, koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.
Non resta saldo l'uomo con l'empietà, ma la radice dei giusti non sarà smossa.
4 Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
La donna perfetta è la corona del marito, ma quella che lo disonora è come carie nelle sue ossa.
5 Maganizo a anthu olungama ndi owongoka, koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.
I pensieri dei giusti sono equità, i propositi degli empi sono frode.
6 Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa, koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.
Le parole degli empi sono agguati sanguinari, ma la bocca degli uomini retti vi si sottrarrà.
7 Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika, koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.
Gli empi, una volta abbattuti, più non sono, ma la casa dei giusti sta salda.
8 Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake, koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.
Un uomo è lodato per il senno, chi ha un cuore perverso è disprezzato.
9 Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika, kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.
Un uomo di poco conto che basta a se stesso vale più di un uomo esaltato a cui manca il pane.
10 Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake, koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.
Il giusto ha cura del suo bestiame, ma i sentimenti degli empi sono spietati.
11 Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.
Chi coltiva la sua terra si sazia di pane, chi insegue chimere è privo di senno.
12 Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa, koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.
Le brame dell'empio sono una rete di mali, la radice dei giusti produce frutti.
13 Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa; koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.
Nel peccato delle sue labbra si impiglia il malvagio, ma il giusto sfuggirà a tale angoscia.
14 Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.
Ognuno si sazia del frutto della sua bocca, ma ciascuno sarà ripagato secondo le sue opere.
15 Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino, koma munthu wanzeru amamvera malangizo.
Lo stolto giudica diritta la sua condotta, il saggio, invece, ascolta il consiglio.
16 Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo, koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.
Lo stolto manifesta subito la sua collera, l'accorto dissimula l'offesa.
17 Woyankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yabodza imafotokoza zonama.
Chi aspira alla verità proclama la giustizia, il falso testimone proclama l'inganno.
18 Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga, koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
V'è chi parla senza riflettere: trafigge come una spada; ma la lingua dei saggi risana.
19 Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa.
La bocca verace resta ferma per sempre, la lingua bugiarda per un istante solo.
20 Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo; koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.
Amarezza è nel cuore di chi trama il male, gioia hanno i consiglieri di pace.
21 Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama, koma munthu woyipa mavuto samuthera.
Al giusto non può capitare alcun danno, gli empi saranno pieni di mali.
22 Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
Le labbra menzognere sono un abominio per il Signore che si compiace di quanti agiscono con sincerità.
23 Munthu wochenjera amabisa nzeru zake, koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.
L'uomo accorto cela il sapere, il cuore degli stolti proclama la stoltezza.
24 Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira, koma aulesi adzakhala ngati kapolo.
La mano operosa ottiene il comando, quella pigra sarà per il lavoro forzato.
25 Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu, koma mawu abwino amamusangalatsa.
L'affanno deprime il cuore dell'uomo, una parola buona lo allieta.
26 Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake, koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.
Il giusto è guida per il suo prossimo, ma la via degli empi fa smarrire.
27 Munthu waulesi sapeza chimene akufuna, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.
Il pigro non troverà selvaggina; la diligenza è per l'uomo un bene prezioso.
28 Mʼnjira yachilungamo muli moyo; koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.
Nella strada della giustizia è la vita, il sentiero dei perversi conduce alla morte.