< Miyambo 11 >

1 Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
מאזני מרמה תועבת יהוה ואבן שלמה רצונו
2 Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
בא-זדון ויבא קלון ואת-צנועים חכמה
3 Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
תמת ישרים תנחם וסלף בגדים ושדם (ישדם)
4 Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
לא-יועיל הון ביום עברה וצדקה תציל ממות
5 Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo, koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.
צדקת תמים תישר דרכו וברשעתו יפל רשע
6 Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa, koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.
צדקת ישרים תצילם ובהות בגדים ילכדו
7 Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso. Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.
במות אדם רשע תאבד תקוה ותוחלת אונים אבדה
8 Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto, koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.
צדיק מצרה נחלץ ויבא רשע תחתיו
9 Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake, koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.
בפה--חנף ישחת רעהו ובדעת צדיקים יחלצו
10 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera, ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.
בטוב צדיקים תעלץ קריה ובאבד רשעים רנה
11 Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima, koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.
בברכת ישרים תרום קרת ובפי רשעים תהרס
12 Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru, koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.
בז-לרעהו חסר-לב ואיש תבונות יחריש
13 Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi; koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.
הולך רכיל מגלה-סוד ונאמן-רוח מכסה דבר
14 Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.
באין תחבלות יפל-עם ותשועה ברב יועץ
15 Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.
רע-ירוע כי-ערב זר ושנא תקעים בוטח
16 Mkazi wodekha amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.
אשת-חן תתמך כבוד ועריצים יתמכו-עשר
17 Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.
גמל נפשו איש חסד ועכר שארו אכזרי
18 Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu, koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.
רשע--עשה פעלת-שקר וזרע צדקה שכר אמת
19 Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo, koma wothamangira zoyipa adzafa.
כן-צדקה לחיים ומרדף רעה למותו
20 Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.
תועבת יהוה עקשי-לב ורצונו תמימי דרך
21 Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa, koma anthu olungama adzapulumuka.
יד ליד לא-ינקה רע וזרע צדיקים נמלט
22 Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba, ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.
נזם זהב באף חזיר-- אשה יפה וסרת טעם
23 Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha, koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.
תאות צדיקים אך-טוב תקות רשעים עברה
24 Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.
יש מפזר ונוסף עוד וחשך מישר אך-למחסור
25 Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.
נפש-ברכה תדשן ומרוה גם-הוא יורא
26 Anthu amatemberera womana anzake chakudya, koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.
מנע בר יקבהו לאום וברכה לראש משביר
27 Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo, koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.
שחר טוב יבקש רצון ודרש רעה תבואנו
28 Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota, koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.
בוטח בעשרו הוא יפול וכעלה צדיקים יפרחו
29 Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto, ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.
עכר ביתו ינחל-רוח ועבד אויל לחכם-לב
30 Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo, ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.
פרי-צדיק עץ חיים ולקח נפשות חכם
31 Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi, kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!
הן צדיק בארץ ישלם אף כי-רשע וחוטא

< Miyambo 11 >