< Miyambo 10 >

1 Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
所羅門的箴言: 智慧之子使父親歡樂; 愚昧之子叫母親擔憂。
2 Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
不義之財毫無益處; 惟有公義能救人脫離死亡。
3 Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.
耶和華不使義人受飢餓; 惡人所欲的,他必推開。
4 Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.
手懶的,要受貧窮; 手勤的,卻要富足。
5 Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru, koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.
夏天聚斂的,是智慧之子; 收割時沉睡的,是貽羞之子。
6 Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama, koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.
福祉臨到義人的頭; 強暴蒙蔽惡人的口。
7 Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso, koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.
義人的紀念被稱讚; 惡人的名字必朽爛。
8 Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.
心中智慧的,必受命令; 口裏愚妄的,必致傾倒。
9 Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
行正直路的,步步安穩; 走彎曲道的,必致敗露。
10 Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto, koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.
以眼傳神的,使人憂患; 口裏愚妄的,必致傾倒。
11 Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo, koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
義人的口是生命的泉源; 強暴蒙蔽惡人的口。
12 Udani umawutsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
恨能挑啟爭端; 愛能遮掩一切過錯。
13 Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu, koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.
明哲人嘴裏有智慧; 無知人背上受刑杖。
14 Anzeru amasunga chidziwitso koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
智慧人積存知識; 愚妄人的口速致敗壞。
15 Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.
富戶的財物是他的堅城; 窮人的貧乏是他的敗壞。
16 Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama, koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.
義人的勤勞致生; 惡人的進項致死。
17 Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo, koma wonyoza chidzudzulo amasochera.
謹守訓誨的,乃在生命的道上; 違棄責備的,便失迷了路。
18 Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.
隱藏怨恨的,有說謊的嘴; 口出讒謗的,是愚妄的人。
19 Mawu akachuluka zolakwa sizisowa, koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
多言多語難免有過; 禁止嘴唇是有智慧。
20 Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.
義人的舌乃似高銀; 惡人的心所值無幾。
21 Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
義人的口教養多人; 愚昧人因無知而死亡。
22 Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
耶和華所賜的福使人富足, 並不加上憂慮。
23 Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa, koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
愚妄人以行惡為戲耍; 明哲人卻以智慧為樂。
24 Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira; chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.
惡人所怕的,必臨到他; 義人所願的,必蒙應允。
25 Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa, koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.
暴風一過,惡人歸於無有; 義人的根基卻是永久。
26 Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso, ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.
懶惰人叫差他的人 如醋倒牙,如煙薰目。
27 Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo; koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.
敬畏耶和華使人日子加多; 但惡人的年歲必被減少。
28 Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe, koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.
義人的盼望必得喜樂; 惡人的指望必致滅沒。
29 Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino, koma wochita zoyipa adzawonongeka.
耶和華的道是正直人的保障, 卻成了作孽人的敗壞。
30 Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.
義人永不挪移; 惡人不得住在地上。
31 Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru, koma lilime lokhota lidzadulidwa.
義人的口滋生智慧; 乖謬的舌必被割斷。
32 Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula, koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.
義人的嘴能令人喜悅; 惡人的口說乖謬的話。

< Miyambo 10 >