< Afilipi 2 >
1 Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo,
2 tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso.
3 Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.
4 Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
5 Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:
6 Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
7 Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
8 Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!
9 Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.
12 Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera,
13 pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.
14 Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo,
15 kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba
16 powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe.
17 Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse.
18 Chomwechonso, inu khalani okondwa ndi osangalala nane pamodzi.
19 Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko, kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu.
20 Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu.
21 Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu.
22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake.
23 Choncho ndikuyembekezera kumutuma msanga ndikangodziwa mmene zinthu zanga ziyendere.
24 Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa.
25 Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga.
26 Pakuti akukulakalakani nonsenu ndipo akusauka mu mtima chifukwa munamva kuti akudwala.
27 Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke.
28 Choncho khumbo langa lofulumiza kumutumiza lakula, kuti pamene mumuonenso musangalale komanso kuti nkhawa yanga ichepe.
29 Mulandireni mwa Ambuye ndi chimwemwe chachikulu, ndipo anthu onga iyeyu muziwachitira ulemu.
30 Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.