< Filemoni 1 >

1 Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu. Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu.
παυλος δεσμιος χριστου ιησου και τιμοθεος ο αδελφος φιλημονι τω αγαπητω και συνεργω ημων
2 Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu.
και απφια τη αγαπητη και αρχιππω τω συστρατιωτη ημων και τη κατ οικον σου εκκλησια
3 Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
χαρις υμιν και ειρηνη απο θεου πατρος ημων και κυριου ιησου χριστου
4 Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga.
ευχαριστω τω θεω μου παντοτε μνειαν σου ποιουμενος επι των προσευχων μου
5 Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse.
ακουων σου την αγαπην και την πιστιν ην εχεις προς τον κυριον ιησουν και εις παντας τους αγιους
6 Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu.
οπως η κοινωνια της πιστεως σου ενεργης γενηται εν επιγνωσει παντος αγαθου του εν υμιν εις χριστον ιησουν
7 Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye.
χαριν γαρ εχομεν πολλην και παρακλησιν επι τη αγαπη σου οτι τα σπλαγχνα των αγιων αναπεπαυται δια σου αδελφε
8 Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita,
διο πολλην εν χριστω παρρησιαν εχων επιτασσειν σοι το ανηκον
9 komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu,
δια την αγαπην μαλλον παρακαλω τοιουτος ων ως παυλος πρεσβυτης νυνι δε και δεσμιος ιησου χριστου
10 ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo.
παρακαλω σε περι του εμου τεκνου ον εγεννησα εν τοις δεσμοις μου ονησιμον
11 Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso.
τον ποτε σοι αχρηστον νυνι δε σοι και εμοι ευχρηστον ον ανεπεμψα
12 Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni.
συ δε αυτον τουτεστιν τα εμα σπλαγχνα προσλαβου
13 Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino.
ον εγω εβουλομην προς εμαυτον κατεχειν ινα υπερ σου διακονη μοι εν τοις δεσμοις του ευαγγελιου
14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza.
χωρις δε της σης γνωμης ουδεν ηθελησα ποιησαι ινα μη ως κατα αναγκην το αγαθον σου η αλλα κατα εκουσιον
15 Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. (aiōnios g166)
ταχα γαρ δια τουτο εχωρισθη προς ωραν ινα αιωνιον αυτον απεχης (aiōnios g166)
16 Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.
ουκετι ως δουλον αλλ υπερ δουλον αδελφον αγαπητον μαλιστα εμοι ποσω δε μαλλον σοι και εν σαρκι και εν κυριω
17 Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo.
ει ουν εμε εχεις κοινωνον προσλαβου αυτον ως εμε
18 Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo.
ει δε τι ηδικησεν σε η οφειλει τουτο εμοι ελλογει
19 Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo.
εγω παυλος εγραψα τη εμη χειρι εγω αποτισω ινα μη λεγω σοι οτι και σεαυτον μοι προσοφειλεις
20 Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu.
ναι αδελφε εγω σου οναιμην εν κυριω αναπαυσον μου τα σπλαγχνα εν κυριω
21 Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.
πεποιθως τη υπακοη σου εγραψα σοι ειδως οτι και υπερ ο λεγω ποιησεις
22 Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.
αμα δε και ετοιμαζε μοι ξενιαν ελπιζω γαρ οτι δια των προσευχων υμων χαρισθησομαι υμιν
23 Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni.
ασπαζονται σε επαφρας ο συναιχμαλωτος μου εν χριστω ιησου
24 Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.
μαρκος αρισταρχος δημας λουκας οι συνεργοι μου
25 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.
η χαρις του κυριου ημων ιησου χριστου μετα του πνευματος υμων αμην [προς φιλημονα εγραφη απο ρωμης δια ονησιμου οικετου]

< Filemoni 1 >