< Numeri 5 >
1 Yehova anawuza Mose kuti,
耶和华晓谕摩西说:
2 “Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa.
“你吩咐以色列人,使一切长大麻风的,患漏症的,并因死尸不洁净的,都出营外去。
3 Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.”
无论男女都要使他们出到营外,免得污秽他们的营;这营是我所住的。”
4 Aisraeli anachitadi zimenezi. Anawatulutsira kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.
以色列人就这样行,使他们出到营外。耶和华怎样吩咐摩西,以色列人就怎样行了。
6 “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene mwamuna kapena mayi walakwira mnzake mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Munthuyo ndi wochimwa ndithu ndipo
“你晓谕以色列人说:无论男女,若犯了人所常犯的罪,以致干犯耶和华,那人就有了罪。
7 ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo.
他要承认所犯的罪,将所亏负人的,如数赔还,另外加上五分之一,也归与所亏负的人。
8 Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake.
那人若没有亲属可受所赔还的,那所赔还的就要归与服事耶和华的祭司;至于那为他赎罪的公羊是在外。
9 Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo.
以色列人一切的圣物中,所奉给祭司的举祭都要归与祭司。
10 Mphatso zilizonse zopatulika ndi za munthuyo, koma zomwe wapereka kwa wansembe ndi za wansembeyo.’”
各人所分别为圣的物,无论是什么,都要归给祭司。”
11 Kenaka Yehova anawuza Mose kuti,
耶和华对摩西说:
12 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mkazi wa munthu wina ayenda njira yosayenera nakhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake,
“你晓谕以色列人说:人的妻若有邪行,得罪她丈夫,
13 nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita),
有人与她行淫,事情严密,瞒过她丈夫,而且她被玷污,没有作见证的人,当她行淫的时候也没有被捉住,
14 mwamuna wake ndi kuyamba kuchita nsanje ndi kukayikira mkazi wakeyo kuti ndi wodetsedwa, komanso ngati amuchitira nsanje ndi kumukayikira ngakhale asanadzidetse,
她丈夫生了疑恨的心,疑恨她,她是被玷污,或是她丈夫生了疑恨的心,疑恨她,她并没有被玷污,
15 apite naye mkaziyo kwa wansembe. Ndipo popita atengenso gawo lakhumi la chopereka chaufa wa barele wokwana kilogalamu imodzi mʼmalo mwa mkaziyo. Asathire mafuta pa nsembeyo kapena lubani, chifukwa ndi nsembe ya chopereka ya chakudya yopereka chifukwa cha nsanje, nsembe yozindikiritsa tchimo.’”
这人就要将妻送到祭司那里,又为她带着大麦面伊法十分之一作供物,不可浇上油,也不可加上乳香;因为这是疑恨的素祭,是思念的素祭,使人思念罪孽。
16 “‘Wansembe abwere naye mkaziyo ndi kumuyimitsa pamaso pa Yehova.
“祭司要使那妇人近前来,站在耶和华面前。
17 Ndipo wansembeyo atenge madzi oyera mʼmbiya ya dothi ndi kuyika mʼmadzimo fumbi lapansi la mʼTenti ya Msonkhano.
祭司要把圣水盛在瓦器里,又从帐幕的地上取点尘土,放在水中。
18 Wansembe atayimika mkaziyo pamaso pa Yehova, amumasule tsitsi lake, ndipo ayike mʼmanja mwake nsembe yozindikiritsa tchimo, nsembe yachakudya ya nsanje, wansembeyo atanyamula madzi owawa omwe amabweretsa temberero.’
祭司要叫那妇人蓬头散发,站在耶和华面前,把思念的素祭,就是疑恨的素祭,放在她手中。祭司手里拿着致咒诅的苦水,
19 Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke.
要叫妇人起誓,对她说:‘若没有人与你行淫,也未曾背着丈夫做污秽的事,你就免受这致咒诅苦水的灾。
20 Koma ngati wayenda njira yoyipa uli pa ukwati ndi mwamuna wako ndi kudzidetsa pogonana ndi mwamuna amene si mwamuna wako,’
你若背着丈夫行了污秽的事,在你丈夫以外有人与你行淫,
21 pamenepo wansembe alumbiritse mkaziyo ndi mawu a matemberero ndi kumuwuza kuti, ‘Yehova achititse anthu ako kukutemberera ndi kukunyoza pamene awononga ntchafu yako ndi kutupitsa mimba yako.
(祭司叫妇人发咒起誓,)愿耶和华叫你大腿消瘦,肚腹发胀,使你在你民中被人咒诅,成了誓语;
22 Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’” “Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’”
并且这致咒诅的水入你的肠中,要叫你的肚腹发胀,大腿消瘦。’妇人要回答说:‘阿们,阿们。’
23 “‘Wansembe alembe matemberero amenewa mʼbuku ndi kuwanyika mʼmadzi owawa aja.
“祭司要写这咒诅的话,将所写的字抹在苦水里,
24 Amwetse mkaziyo madzi owawawo omwe amabweretsa temberero, ndipo madzi amenewo adzalowa mʼmimba mwake ndi kuyambitsa ululu woopsa.
又叫妇人喝这致咒诅的苦水;这水要进入她里面变苦了。
25 Wansembe achotse mʼmanja mwa mkaziyo nsembe yachakudya ya nsanje ija, nayiweyula pamaso pa Yehova ndi kuyipereka pa guwa lansembe.
祭司要从妇人的手中取那疑恨的素祭,在耶和华面前摇一摇,拿到坛前;
26 Tsono wansembeyo atapeko ufa dzanja limodzi kuti ukhale wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa lansembe. Atatha izi, amwetse mkaziyo madzi aja.
又要从素祭中取出一把,作为这事的纪念,烧在坛上,然后叫妇人喝这水。
27 Ndipo ngati mkaziyo anadzidetsadi ndi kukhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, pamene amwa madzi obweretsa matemberero aja, nalowa mʼmimba mwake, adzamva ululu woopsa. Mimba yake idzatupa ndi ntchafu yake idzawonongeka ndipo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu ake.
叫她喝了以后,她若被玷污,得罪了丈夫,这致咒诅的水必进入她里面变苦了,她的肚腹就要发胀,大腿就要消瘦,那妇人便要在他民中被人咒诅。
28 Koma ngati mkaziyo sanadzidetse ndi kuti alibe tchimo, adzakhala wopanda mlandu ndipo adzabereka ana.
若妇人没有被玷污,却是清洁的,就要免受这灾,且要怀孕。
29 “‘Limeneli ndiye lamulo la nsanje pamene mkazi wayenda njira yoyipa ndi kudzidetsa ali pa ukwati ndi mwamuna wake,
“妻子背着丈夫行了污秽的事,
30 kapena pamene maganizo a nsanje abwera kwa mwamuna wake chifukwa chokayikira mkazi wakeyo. Wansembe azitenga mkazi wotere ndi kumuyimiritsa pamaso pa Yehova ndipo agwiritse ntchito lamulo lonseli kwa mkaziyo.
或是人生了疑恨的心,疑恨他的妻,就有这疑恨的条例。那时他要叫妇人站在耶和华面前,祭司要在她身上照这条例而行。
31 Mwamunayo adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkaziyo adzasenza zotsatira za tchimo lake.’”
男人就为无罪,妇人必担当自己的罪孽。”