< Numeri 36 >

1 Atsogoleri a mabanja a fuko la Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase omwe anali ochokera ku fuko la ana a Yosefe anabwera ndi kuyankhula ndi Mose, atsogoleri ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli.
ויקרבו ראשי האבות למשפחת בני גלעד בן מכיר בן מנשה--ממשפחת בני יוסף וידברו לפני משה ולפני הנשאים--ראשי אבות לבני ישראל
2 Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi.
ויאמרו את אדני צוה יהוה לתת את הארץ בנחלה בגורל לבני ישראל ואדני צוה ביהוה לתת את נחלת צלפחד אחינו לבנתיו
3 Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa.
והיו לאחד מבני שבטי בני ישראל לנשים ונגרעה נחלתן מנחלת אבתינו ונוסף על נחלת המטה אשר תהיינה להם ומגרל נחלתנו יגרע
4 Pamene chaka cha chikondwerero cha zaka makumi asanu, cha Aisraeli chafika, cholowa chawo chidzawonjezeredwa ku fuko limene iwo akwatiwako. Ndipo katundu wawo adzachotsedwa pa cholowa cha fuko la makolo athu.”
ואם יהיה היבל לבני ישראל ונוספה נחלתן על נחלת המטה אשר תהיינה להם ומנחלת מטה אבתינו יגרע נחלתן
5 Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona.
ויצו משה את בני ישראל על פי יהוה לאמר כן מטה בני יוסף דברים
6 Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo
זה הדבר אשר צוה יהוה לבנות צלפחד לאמר לטוב בעיניהם תהיינה לנשים אך למשפחת מטה אביהם--תהיינה לנשים
7 kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake.
ולא תסב נחלה לבני ישראל ממטה אל מטה כי איש בנחלת מטה אבתיו ידבקו בני ישראל
8 Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake.
וכל בת ירשת נחלה ממטות בני ישראל--לאחד ממשפחת מטה אביה תהיה לאשה למען יירשו בני ישראל איש נחלת אבתיו
9 Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.”
ולא תסב נחלה ממטה למטה אחר כי איש בנחלתו ידבקו מטות בני ישראל
10 Choncho ana aakazi a Zelofehadi anachita monga Yehova analamulira Mose.
כאשר צוה יהוה את משה כן עשו בנות צלפחד
11 Ana aakazi a Zelofehadi amene ndi Mahila, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, anakwatiwa ndi asuweni awo a ku mbali ya abambo awo.
ותהיינה מחלה תרצה וחגלה ומלכה ונעה--בנות צלפחד לבני דדיהן לנשים
12 Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo.
ממשפחת בני מנשה בן יוסף היו לנשים ותהי נחלתן על מטה משפחת אביהן
13 Awa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kupyolera mwa Mose ku chigwa cha Mowabu mʼmbali mwa Yorodani, ku Yeriko.
אלה המצות והמשפטים אשר צוה יהוה ביד משה--אל בני ישראל בערבת מואב על ירדן ירחו

< Numeri 36 >