< Numeri 34 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
And the Lord said to Moses,
2 “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
Give orders to the children of Israel and say to them, When you come into the land of Canaan; (this is the land which is to be your heritage, the land of Canaan inside these limits, )
3 “‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere.
Then your south quarter will be from the waste land of Zin by the side of Edom, and your limit on the south will be from the east end of the Salt Sea,
4 Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni,
And round to the south of the slope of Akrabbim, and on to Zin: and its direction will be south of Kadesh-barnea, and it will go as far as Hazar-addar and on to Azmon:
5 kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
And from Azmon it will go round to the stream of Egypt as far as the sea.
6 “‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
And for your limit on the west you will have the Great Sea and its edge: this will be your limit on the west.
7 “‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori
And your limit on the north will be the line from the Great Sea to Mount Hor:
8 ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi,
And from Mount Hor the line will go in the direction of Hamath; the farthest point of it will be at Zedad:
9 ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
And the limit will go on to Ziphron, with its farthest point at Hazar-enan: this will be your limit on the north.
10 “‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu.
And on the east, your limit will be marked out from Hazar-enan to Shepham,
11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti.
Going down from Shepham to Riblah on the east side of Ain, and on as far as the east side of the sea of Chinnereth:
12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. “‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’”
And so down to Jordan, stretching to the Salt Sea: all the land inside these limits will be yours.
13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka,
And Moses gave orders to the children of Israel saying, This is the land which is to be your heritage, by the decision of the Lord, which by the Lord's order is to be given to the nine tribes and the half-tribe:
14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo.
For the tribe of the children of Reuben, by their fathers' families, and the tribe of the children of Gad, by their fathers' families, and the half-tribe of Manasseh, have been given their heritage:
15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
The two tribes and the half-tribe have been given their heritage on the other side of Jordan at Jericho, on the east looking to the dawn.
16 Yehova anawuza Mose kuti,
And the Lord said to Moses,
17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni.
These are the names of the men who are to make the distribution of the land among you: Eleazar the priest and Joshua, the son of Nun.
18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo.
And you are to take one chief from every tribe to make the distribution of the land.
19 Mayina awo ndi awa: Kalebe mwana wa Yefune, wochokera ku fuko la Yuda,
And these are the names of the men: of the tribe of Judah, Caleb, the son of Jephunneh.
20 Semueli mwana wa Amihudi, wochokera ku fuko la Simeoni;
And of the tribe of the children of Simeon, Shemuel, the son of Ammihud.
21 Elidadi mwana wa Kisiloni, wochokera ku fuko la Benjamini;
Of the tribe of Benjamin, Elidad, the son of Chislon.
22 Buki mwana wa Yogili, mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
And of the tribe of the children of Dan, a chief, Bukki, the son of Jogli.
23 Hanieli mwana wa Efodi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
Of the children of Joseph: of the tribe of the children of Manasseh, a chief, Hanniel, the son of Ephod:
24 Kemueli mwana wa Sifitani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
And of the tribe of the children of Ephraim, a chief, Kemuel, the son of Shiphtan.
25 Elizafani mwana wa Parinaki, mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
And of the tribe of the children of Zebulun, a chief, Elizaphan, the son of Parnach.
26 Palitieli mwana wa Azani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
And of the tribe of the children of Issachar, a chief, Paltiel, the son of Azzan.
27 Ahihudi mwana wa Selomi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
And of the tribe of the children of Asher, a chief, Ahihud, the son of Shelomi.
28 Pedaheli mwana wa Amihudi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
And of the tribe of the children of Naphtali, a chief, Pedahel, the son of Ammihud.
29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.
These are they to whom the Lord gave orders to make the distribution of the heritage among the children of Israel in the land of Canaan.

< Numeri 34 >