< Numeri 33 >
1 Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni.
These were the movements of the people of Israel after they left the land of Egypt by their armed groups under the leadership of Moses and Aaron.
2 Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa:
Moses wrote down the places from where they left to where they went, as commanded by Yahweh. These were their movements, departure after departure.
3 Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona,
They traveled from Rameses during the first month, leaving on the fifteenth day of the first month. On the morning after the Passover, the people of Israel left openly, in the sight of all the Egyptians.
4 pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.
This happened while the Egyptians were burying all their firstborn, those whom Yahweh had killed among them, for he also inflicted punishment on their gods.
5 Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti.
The people of Israel set out from Rameses and camped at Succoth.
6 Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu.
They set out from Succoth and camped at Etham, on the edge of the wilderness.
7 Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.
They set out from Etham and turned back to Pi Hahiroth, which is opposite Baal Zephon, where they camped opposite Migdol.
8 Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara.
Then they set out from opposite Pi Hahiroth and passed through the middle of the sea into the wilderness. They traveled three days' journey into the wilderness of Etham and camped at Marah.
9 Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.
They set out from Marah and arrived at Elim. At Elim were twelve springs of water and seventy palm trees. That is where they camped.
10 Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.
They set out from Elim and camped by the Sea of Reeds.
11 Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini.
They set out from the Sea of Reeds and camped in the wilderness of Sin.
12 Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika.
They set out from the wilderness of Sin and camped at Dophkah.
13 Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi.
They set out from Dophkah and camped at Alush.
14 Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa.
They set out from Alush and camped at Rephidim, where no water was found for the people to drink.
15 Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai
They set out from Rephidim and camped in the wilderness of Sinai.
16 Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava.
They set out from the wilderness of Sinai and camped at Kibroth Hattaavah.
17 Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti.
They set out from Kibroth Hattaavah and camped at Hazeroth.
18 Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima.
They set out from Hazeroth and camped at Rithmah.
19 Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi.
They set out from Rithmah and camped at Rimmon Perez.
20 Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina.
They set out from Rimmon Perez and camped at Libnah.
21 Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa.
They set out from Libnah and camped at Rissah.
22 Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata.
They set out from Rissah and camped at Kehelathah.
23 Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi.
They set out from Kehelathah and camped at Mount Shepher.
24 Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada.
They set out from Mount Shepher and camped at Haradah.
25 Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti.
They set out from Haradah and camped at Makheloth.
26 Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati.
They set out from Makheloth and camped at Tahath.
27 Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera.
They set out from Tahath and camped at Terah.
28 Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika.
They set out from Terah and camped at Mithkah.
29 Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona.
They set out from Mithkah and camped at Hashmonah.
30 Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti.
They set out from Hashmonah and camped at Moseroth.
31 Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani.
They set out from Moseroth and camped at Bene Jaakan.
32 Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi.
They set out from Bene Jaakan and camped at Hor Haggidgad.
33 Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata.
They set out from Hor Haggidgad and camped at Jotbathah.
34 Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona.
They set out from Jotbathah and camped at Abronah.
35 Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi.
They set out from Abronah and camped at Ezion Geber.
36 Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi.
They set out from Ezion Geber and camped in the wilderness of Zin at Kadesh.
37 Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu.
They set out from Kadesh and camped at Mount Hor, at the edge of the land of Edom.
38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
Aaron the priest went up Mount Hor at Yahweh's command and died there in the fortieth year after the people of Israel had come out of the land of Egypt, in the fifth month, on the first day of the month.
39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.
Aaron was a 123 years old when he died on Mount Hor.
40 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera.
The Canaanite, the king of Arad, who lived in the southern wilderness in the land of Canaan, heard of the coming of the people of Israel.
41 Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni.
They set out from Mount Hor and camped at Zalmonah.
42 Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni.
They set out from Zalmonah and camped at Punon.
43 Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti.
They set out from Punon and camped at Oboth.
44 Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu.
They set out from Oboth and camped at Iye Abarim, on the border of Moab.
45 Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi.
They set out from Iye Abarim and camped at Dibon Gad.
46 Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu.
They set out from Dibon Gad and camped at Almon Diblathaim.
47 Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo.
They set out from Almon Diblathaim and camped in the mountains of Abarim, opposite Nebo.
48 Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko.
They set out from the mountains of Abarim and camped in the plains of Moab by the Jordan at Jericho.
49 Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu.
They camped by the Jordan, from Beth Jeshimoth to Abel Shittim in the plains of Moab.
50 Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti,
Yahweh spoke to Moses in the plains of Moab by the Jordan at Jericho and said,
51 “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani,
“Speak to the people of Israel and say to them, 'When you cross over the Jordan into the land of Canaan,
52 mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo.
then you must drive out all the land's inhabitants before you. You must destroy all their carved figures. You must destroy all their cast figures and demolish all their high places.
53 Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo.
You must take possession of the land and settle in it, because I have given you the land to possess.
54 Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.
You must inherit the land by lot, according to each clan. To the larger clans you must give a larger share of land, and to the smaller clans you must give a smaller share of land. Wherever the lot falls to each clan, that land will belong to it. You will inherit the land according to your ancestors' tribes.
55 “‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo.
But if you do not drive out the land's inhabitants before you, then the people you allow to stay will become like objects in your eyes and thorns in your sides. They will make your lives difficult in the land where you settle.
56 Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’”
Then it will happen that what I now intend to do to those people, I will do also to you.'”