< Numeri 32 >

1 Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo.
Now the children of Reuben and the children of Gad had a very great multitude of livestock. They saw the land of Jazer, and the land of Gilead. Behold, the place was a place for livestock.
2 Choncho Arubeni ndi Agadi anapita kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa atsogoleri a anthu ndi kunena kuti,
Then the children of Gad and the children of Reuben came and spoke to Moses, and to Eleazar the priest, and to the princes of the congregation, saying,
3 “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni,
“Ataroth, Dibon, Jazer, Nimrah, Heshbon, Elealeh, Sebam, Nebo, and Beon,
4 dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto.
the land which The LORD struck before the congregation of Israel, is a land for livestock; and your servants have livestock.”
5 Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’”
They said, “If we have found favour in your sight, let this land be given to your servants for a possession. Don’t bring us over the Jordan.”
6 Ndipo Mose anati kwa Agadi ndi Arubeni, “Kodi anthu a mtundu wanu apite ku nkhondo inu mutangokhala kuno?
Moses said to the children of Gad, and to the children of Reuben, “Shall your brothers go to war while you sit here?
7 Chifukwa chiyani mukufowoketsa Aisraeli kupita mʼdziko limene Yehova wawapatsa?
Why do you discourage the heart of the children of Israel from going over into the land which the LORD has given them?
8 Izi ndi zimene makolo anu anachita pamene ndinawatuma kuchokera ku Kadesi kukaona dzikolo.
Your fathers did so when I sent them from Kadesh Barnea to see the land.
9 Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa.
For when they went up to the valley of Eshcol, and saw the land, they discouraged the heart of the children of Israel, that they should not go into the land which the LORD had given them.
10 Yehova anakwiya tsiku limenelo ndipo analumbira kuti,
The LORD’s anger burnt in that day, and he swore, saying,
11 ‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
‘Surely none of the men who came up out of Egypt, from twenty years old and upward, shall see the land which I swore to Abraham, to Isaac, and to Jacob; because they have not wholly followed me,
12 Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’
except Caleb the son of Jephunneh the Kenizzite, and Joshua the son of Nun, because they have followed the LORD completely.’
13 Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha.
The LORD’s anger burnt against Israel, and he made them wander back and forth in the wilderness forty years, until all the generation who had done evil in the LORD’s sight was consumed.
14 “Ndipo onani tsopano, inu mʼbado wochimwa, mwalowa mʼmalo mwa makolo anu ndipo mwachititsa kuti Yehova akwiyire Israeli kwambiri.
“Behold, you have risen up in your fathers’ place, an increase of sinful men, to increase the fierce anger of the LORD towards Israel.
15 Ngati muleka kumutsata, Iye adzawasiyiranso anthu onsewa mʼchipululu ndipo mudzawonongetsa anthu onsewa.”
For if you turn away from after him, he will yet again leave them in the wilderness; and you will destroy all these people.”
16 Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu.
They came near to him, and said, “We will build sheepfolds here for our livestock, and cities for our little ones;
17 Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli.
but we ourselves will be ready armed to go before the children of Israel, until we have brought them to their place. Our little ones shall dwell in the fortified cities because of the inhabitants of the land.
18 Sitidzabwerera ku midzi yathu mpaka Mwisraeli aliyense atalandira cholowa chake.
We will not return to our houses until the children of Israel have all received their inheritance.
19 Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.”
For we will not inherit with them on the other side of the Jordan and beyond, because our inheritance has come to us on this side of the Jordan eastward.”
20 Tsono Mose anati kwa anthuwo, “Ngati inu mudzachita zimenezi, kutenga zida zankhondo pamaso pa Yehova kuti muchite nkhondo,
Moses said to them: “If you will do this thing, if you will arm yourselves to go before the LORD to the war,
21 ndipo ngati nonsenu mudzapita ndi zida kuwoloka Yorodani pamaso pa Yehova mpaka atachotsa adani ake pamaso pake,
and every one of your armed men will pass over the Jordan before the LORD until he has driven out his enemies from before him,
22 dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.
and the land is subdued before the LORD; then afterward you shall return, and be clear of obligation to the LORD and to Israel. Then this land shall be your possession before the LORD.
23 “Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani.
“But if you will not do so, behold, you have sinned against the LORD; and be sure your sin will find you out.
24 Amangireni akazi ndi ana anu mizinda, mangani makola a ziweto zanu, koma chitani zomwe mwalonjeza.”
Build cities for your little ones, and folds for your sheep; and do that which has proceeded out of your mouth.”
25 Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira.
The children of Gad and the children of Reuben spoke to Moses, saying, “Your servants will do as my lord commands.
26 Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi,
Our little ones, our wives, our flocks, and all our livestock shall be there in the cities of Gilead;
27 koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.”
but your servants will pass over, every man who is armed for war, before the LORD to battle, as my lord says.”
28 Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli.
So Moses commanded concerning them to Eleazar the priest, and to Joshua the son of Nun, and to the heads of the fathers’ households of the tribes of the children of Israel.
29 Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo.
Moses said to them, “If the children of Gad and the children of Reuben will pass with you over the Jordan, every man who is armed to battle before the LORD, and the land is subdued before you, then you shall give them the land of Gilead for a possession;
30 Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani.
but if they will not pass over with you armed, they shall have possessions amongst you in the land of Canaan.”
31 Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena.
The children of Gad and the children of Reuben answered, saying, “As the LORD has said to your servants, so will we do.
32 Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.”
We will pass over armed before the LORD into the land of Canaan, and the possession of our inheritance shall remain with us beyond the Jordan.”
33 Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira.
Moses gave to them, even to the children of Gad, and to the children of Reuben, and to the half-tribe of Manasseh the son of Joseph, the kingdom of Sihon king of the Amorites, and the kingdom of Og king of Bashan; the land, according to its cities and borders, even the cities of the surrounding land.
34 Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri,
The children of Gad built Dibon, Ataroth, Aroer,
35 Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha,
Atroth-shophan, Jazer, Jogbehah,
36 Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo.
Beth Nimrah, and Beth Haran: fortified cities and folds for sheep.
37 Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu,
The children of Reuben built Heshbon, Elealeh, Kiriathaim,
38 Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo.
Nebo, and Baal Meon, (their names being changed), and Sibmah. They gave other names to the cities which they built.
39 Zidzukulu za Makiri mwana wa Manase zinapita ku Giliyadi kulanda mzindawo ndi kuthamangitsira kunja Aamori omwe anali kumeneko.
The children of Machir the son of Manasseh went to Gilead, took it, and dispossessed the Amorites who were therein.
40 Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko.
Moses gave Gilead to Machir the son of Manasseh; and he lived therein.
41 Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi.
Jair the son of Manasseh went and took its villages, and called them Havvoth Jair.
42 Ndipo Noba analanda Kenati ndi midzi yozungulira ndi kuyitcha Noba, kutengera dzina la iye mwini.
Nobah went and took Kenath and its villages, and called it Nobah, after his own name.

< Numeri 32 >