< Numeri 30 >

1 Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi:
Moïse parla aux chefs des tribus des enfants d’Israël, en ces termes: "Voici ce qu’a ordonné l’Éternel:
2 Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena.
Si un homme fait un vœu au Seigneur, ou s’impose, par un serment, quelque interdiction à lui-même, il ne peut violer sa parole: tout ce qu’a proféré sa bouche, il doit l’accomplir.
3 “Pamene munthu wamkazi amene akukhalabe mʼnyumba ya abambo ake alumbira kwa Yehova kuti adzachita zimene walonjeza pa ubwana wake,
Pour la femme, si elle fait un vœu au Seigneur ou s’impose une abstinence dans la maison de son père, pendant sa jeunesse,
4 abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija.
et que son père, ayant connaissance de son vœu ou de l’abstinence qu’elle s’est imposée, garde le silence vis-à-vis d’elle, ses vœux, quels qu’ils soient, seront valables; toute abstinence qu’elle a pu s’imposer sera maintenue.
5 Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza.
Mais si son père la désavoue le jour où il en a eu connaissance, tous ses vœux et les interdictions qu’elle a pu s’imposer seront nuls. Le Seigneur lui pardonnera, son père l’ayant désavouée.
6 “Ngati akwatiwa atalumbira kale kapena ngati alonjeza mofulumira ndi pakamwa pake,
Que si elle passe en puissance d’époux étant soumise à des vœux ou à une promesse verbale qui lui impose une abstinence,
7 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma wosanenapo kanthu, mkaziyo achitedi zomwe walumbirazo. Achite ndithu zomwe walonjeza zija.
que son époux l’apprenne à une époque quelconque et garde le silence à son égard, ses vœux seront valables, et les abstinences qu’elle s’est imposées subsisteront.
8 Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira.
Mais si, le jour où il en a eu connaissance, son époux la désavoue, il annule par là le vœu qui la lie ou la parole de ses lèvres qui lui imposait l’abstinence; et le Seigneur lui pardonnera.
9 “Mayi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi.
Quant aux vœux d’une femme veuve ou répudiée, tout ce qu’elle s’est imposé sera obligatoire pour elle.
10 “Koma ngati mayi wokwatiwa alumbira nalonjeza kuti adzachitadi zimene walonjeza,
Au cas où c’est en puissance de mari qu’elle a fait un vœu ou s’est interdit quelque chose par serment;
11 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma osayankhulapo kanthu, osamuletsa, ayenera kuchitadi zonse zimene walumbira ndi zonse zimene walonjeza.
si son époux l’apprend et ne lui dit rien, ne la désavoue point, tous ses vœux et toute abstinence qu’elle a pu s’imposer restent obligatoires.
12 Koma ngati mwamuna wake amva ndi kumuletsa kuti asachite zomwe walumbirazo, palibe lamulo lomukakamiza mayiyo kuchita zomwe walumbirazo kapenanso zimene walonjeza. Popeza mwamuna wake wamuletsa, Yehova adzamukhululukira mayiyo.
Si, au contraire, son époux les annule le jour où il en a eu connaissance, tout ce qu’a proféré sa bouche, soit vœux, soit interdiction personnelle, sera sans effet: son époux les a annulés, Dieu sera indulgent pour elle.
13 Mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana zimene mayiyo walumbira kapena zimene walonjeza zokhudza kudzilanga yekha.
Tout vœu, tout serment d’abstinence, tendant à mortifier la personne, l’époux peut les ratifier ou il peut les rendre nuls.
14 Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira.
Si son époux ne s’en explique pas à elle du jour au lendemain, il sanctionne ses vœux ou les abstinences auxquelles elle s’est soumise, parce qu’il s’est tu lorsqu’il en a eu connaissance.
15 Koma ngati mwamunayo amukaniza patapita kanthawi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa mʼmalo mwa mayiyo.”
Que s’il les invalidait après qu’il en a eu connaissance, sa faute à elle retomberait sur lui."
16 Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo.
Telles sont les règles que l’Éternel avait prescrites à Moïse sur les rapports entre l’homme et sa femme, entre le père et sa fille adolescente dans la maison paternelle.

< Numeri 30 >