< Numeri 3 >
1 Iyi ndi mbiri ya banja la Aaroni ndi Mose pa nthawi yomwe Yehova anayankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.
2 Mayina a ana aamuna a Aaroni anali Nadabu, woyamba kubadwa, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
3 Amenewa ndi mayina a ana aamuna a Aaroni, ansembe odzozedwa omwe anapatulidwa kuti azitumikira ngati ansembe.
4 Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo.
5 Yehova anati kwa Mose,
6 “Bweretsa fuko la Levi ndipo ulipereke kwa Aaroni wansembe kuti lizimutumikira.
7 Azigwira ntchito yothandiza iyeyo ndi gulu lonse ku tenti ya msonkhano pogwira ntchito ya ku Chihema.
8 Azisamalira zipangizo zonse za mu tenti ya msonkhano, ndipo azigwirira ntchito Aisraeli potumikira mu tenti.
9 Pereka Alevi kwa Aaroni ndi kwa ana ake aamuna. Amenewa ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwa iye kwathunthu.
10 Usankhe Aaroni ndi ana ake aamuna kuti azitumikira pa ntchito ya unsembe. Koma wina aliyense woyandikira malo opatulika aphedwe.”
11 Yehova anawuzanso Mose kuti,
12 “Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga,
13 pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.”
14 Yehova anawuza Mose mʼchipululu cha Sinai kuti,
15 “Werenga Alevi monga mwa mabanja awo ndi mafuko awo. Werenga mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kapena kupitirirapo.”
16 Choncho Mose anawawerenga potsatira zomwe Yehova anamulamulira.
17 Mayina a ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
18 Mayina a ana a Geresoni potsata mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simei.
19 Ana a Kohati potsata mabanja awo ndi awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
20 Ana a Merari potsata mabanja awo ndi awa: Mali ndi Musi. Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi monga mwa makolo awo.
21 Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni.
22 Chiwerengero cha amuna onse amene anawawerenga a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 7,500.
23 Mabanja a Ageresoni azimanga misasa yawo kumadzulo, kumbuyo kwa Chihema.
24 Mtsogoleri wa mabanja a Ageresoni anali Eliyasafu mwana wa Laeli.
25 Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano,
26 ndi makatani wotchinga bwalo, katani ya pa chipata cholowera ku bwalo lozungulira Chihema ndi guwa lansembe, zingwe ndi zonse zokhudzana ndi ntchito yawo.
27 Kwa Kohati kunali mabanja a Amramu, Aizihara, Ahebroni ndi Auzieli. Awa ndiye anali mabanja a Akohati.
28 Chiwerengero cha amuna onse a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 8,600. Akohati ankagwira ntchito yosamalira malo wopatulika.
29 Mabanja a ana a Kohati ankamanga misasa yawo kummwera kwa Chihema.
30 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Kohati anali Elizafani mwana wa Uzieli.
31 Iwo ankagwira ntchito yosamalira Bokosi la Chipangano, tebulo, choyikapo nyale, maguwa, zipangizo za kumalo wopatulika zimene ansembe ankagwiritsa ntchito, katani, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito.
32 Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika.
33 Kwa Merari kunali banja la Mali ndi banja la Musi. Amenewa ndiye anali mabanja a Amerari.
34 Chiwerengero cha amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 6,200.
35 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Amerari anali Zuriyeli mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga misasa yawo kumpoto kwa Chihema.
36 Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito,
37 pamodzi ndi mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema ndi zingwe zake.
38 Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa.
39 Alevi onse amene Mose ndi Aaroni anawawerenga potsatira lamulo la Yehova monga mwa magulu a mabanja awo, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo anali 22,000.
40 Yehova anawuza Mose kuti, “Werenga ana onse aamuna oyamba kubadwa mu Israeli, omwe ali ndi mwezi umodzi kapena kupitirirapo ndipo ulembe mndandanda wa mayina awo.
41 Unditengere Alevi onse mʼmalo mwa ana oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso ziweto zazimuna za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa za Aisraeli. Ine ndine Yehova.”
42 Choncho Mose anawerenga ana aamuna onse oyamba kubadwa a Aisraeli monga momwe Yehova anamulamulira.
43 Chiwerengero chonse cha ana aamuna oyamba kubadwa kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 22, 273.
44 Ndipo Yehova anawuzanso Mose kuti,
45 “Tenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso zoweta zonse za Alevi mʼmalo mwa zoweta za Aisraeli. Alevi ndi anga. Ine ndine Yehova.
46 Pofuna kuwombola ana aamuna 273 oyamba kubadwa a Aisraeli amene anaposa chiwerengero cha aamuna a fuko la Levi,
47 utenge masekeli asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale ofanana ndi masekeli a ku malo wopatulika, kumene sekeli imodzi imakwanira magera makumi awiri.
48 Ndalama zimenezi uzipereke kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kuti ukhale mtengo woombolera Aisraeli woonjezerawo.”
49 Choncho Mose anatenga ndalama zowombolera zija kuchokera kwa Aisraeli amene chiwerengero chawo chinaposa chiwerengero cha omwe anawomboledwa ndi Alevi.
50 Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli.
51 Mose anapereka ndalama zowombolera zija kwa Aaroni ndi ana ake aamuna monga mwa mawu amene Yehova analamulira.