< Numeri 29 >

1 “‘Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Ili ndi tsiku limene muziliza malipenga.
“Now the first day of the seventh month also shall be venerable and holy to you. In it, you shall not do any servile work, because it is the day of the sounding of the trumpets.
2 Muzipereka mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi wopanda chilema monga nsembe zopsereza, fungo lokoma kwa Yehova.
And you shall offer a holocaust, as a most sweet odor to the Lord: one calf from the herd, one ram, and seven immaculate one-year-old lambs;
3 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzipereka chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa yayimuna iliyonse muzipereka makilogalamu awiri.
and, as their sacrifices, fine wheat flour sprinkled with oil: three tenths for each calf, two tenths for a ram,
4 Pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja muzipereka kilogalamu imodzi.
one tenth for a lamb, which all together are seven lambs;
5 Muziperekanso mbuzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu.
and a he-goat for sin, which is offered as an expiation for the people,
6 Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.
aside from the holocaust of the first day of the month with its sacrifices, and the perpetual holocaust with the usual libations. By these same ceremonies, you shall offer incense as a most sweet odor to the Lord.
7 “‘Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiriwu, muzichita msonkhano wopatulika. Muzisala zakudya ndipo musamagwire ntchito.
Likewise, the tenth day of this seventh month shall be for you holy and venerable, and you shall afflict your souls. You shall do no servile work in it.
8 Muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma lokondweretsa Yehovayo; ngʼombe yayimuna imodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi. Zimenezi zizikhala zopanda chilema.
And you shall offer a holocaust to the Lord, as a most sweet odor: one calf from the herd, one ram, seven immaculate one-year-old lambs;
9 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri;
and for their sacrifices, fine wheat flour sprinkled with oil: three tenths for each calf, two tenths for a ram,
10 kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiriwo.
one tenth for each lamb, which are all together seven lambs;
11 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo ija, kuwonjezanso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi cha chakumwa.
and a he-goat for sin, apart from those things which are usually offered for offenses as an expiation, and as a perpetual holocaust, with their sacrifice and libations.
12 “‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri.
Yet truly, on the fifteenth day of the seventh month, which shall be for you holy and venerable, you shall not do any servile work in it, but you shall celebrate a solemnity to the Lord for seven days.
13 Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
And you shall offer a holocaust, as a most sweet odor to the Lord: thirteen calves from the herd, two rams, fourteen immaculate one-year-old lambs;
14 Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri.
and as their libations, fine wheat flour sprinkled with oil: three tenths for each calf, which is all together thirteen calves, and two tenths for each ram, that is, all together two rams,
15 Pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa aamuna khumi ndi anayiwo, muzipereka chakudya cha kilogalamu imodzi.
and one tenth for each lamb, which is all together fourteen lambs;
16 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
and a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and the sacrifice and its libation.
17 “‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema.
On the next day, you shall offer twelve calves from the herd, two rams, and fourteen immaculate one-year-old lambs.
18 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
19 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and the sacrifice and its libation.
20 “‘Pa tsiku lachitatu muzipereka ngʼombe zazimuna khumi ndi imodzi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
On the third day, you shall offer eleven calves, two rams, and fourteen immaculate one-year-old lambs.
21 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
22 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and the sacrifice and its libation.
23 “‘Pa tsiku lachinayi muzipereka ngʼombe zazimuna khumi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
On the fourth day, you shall offer ten calves, two rams, and fourteen immaculate one-year-old lambs.
24 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and the libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
25 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and its sacrifice and libation.
26 “‘Pa tsiku lachisanu muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zinayi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
On the fifth day, you shall offer nine calves, two rams, and fourteen immaculate one-year-old lambs.
27 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
28 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and its sacrifice and libation.
29 “‘Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zitatu, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
On the sixth day, you shall offer eight calves, two rams, and fourteen immaculate one-year-old lambs.
30 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
31 Muziperekenso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and its sacrifice and libation.
32 “‘Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa amuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
On the seventh day, you shall offer seven calves, and two rams, and fourteen immaculate one-year-old lambs.
33 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
34 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and its sacrifice and libation.
35 “‘Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
On the eighth day, which is most honored, you shall not do any servile work,
36 Muzipereka chopereka chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ngʼombe imodzi yayimuna, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa amuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
offering a holocaust as a most sweet odor to the Lord: one calf, one ram, and seven immaculate one-year-old lambs.
37 Pamodzi ndi ngʼombe yayimunayo, nkhosa yayimunayo ndi ana ankhosawo, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
And the sacrifices and libations for each of the calves and the rams and the lambs, you shall celebrate according to the rite,
38 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
with a he-goat for sin, apart from the perpetual holocaust, and its sacrifice and libation.
39 “‘Kuwonjezera pa zopereka zimene munalumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu, muzipereka zimenezi kwa Yehova pa masiku osankhika a chikondwerero chanu. Nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.’”
These things you shall offer to the Lord in your solemnities, aside from the vowed and voluntary oblations, as a holocaust, as a sacrifice, as a libation, or as peace-offering victims.”
40 Mose anawuza Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamulira.
And Moses explained to the sons of Israel all that the Lord had commanded him.

< Numeri 29 >