< Numeri 28 >
1 Yehova anawuza Mose kuti,
El Señor le dijo a Moisés:
2 “Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’
“Dales las siguientes normas a los israelitas: Debes presentarme en el momento apropiado mis ofrendas de comida para que las acepte.
3 Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema.
Diles que debes presentar al Señor cada día dos corderos machos de un año como holocausto continua.
4 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo.
Ofrece un cordero por la mañana y otro por la tarde antes de que oscurezca,
5 Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi.
junto con una décima parte de una efa de la mejor harina para una ofrenda de grano, mezclada con un cuarto de hin de aceite de oliva prensado.
6 Iyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku imene analamula pa phiri la Sinai kuti ikhale fungo lokoma, nsembe yopsereza pa moto yopereka kwa Yehova.
“Este es un holocausto continuo que se inició en el Monte Sinaí como una ofrenda aceptable para el Señor.
7 Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova.
La ofrenda de bebida que acompaña a cada cordero debe ser un cuarto de hin. Vierte la ofrenda de bebida fermentada al Señor en el santuario.
8 Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’”
Ofrecerás el segundo cordero por la tarde antes de que oscurezca, junto con las mismas ofrendas de grano y bebida que por la mañana. Es un holocausto aceptable para el Señor.
9 “‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta.
“En el día de reposo, presentarás los corderos machos de dos años, sin defectos, junto con una ofrenda de grano de dos décimas de efa de la mejor harina mezclada con aceite de oliva, y su libación.
10 Iyi ndi nsembe yopsereza ya pa Sabata iliyonse, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake chachakumwa.’”
Este holocausto debe ser presentado cada sábado además del holocausto continuo y su libación.
11 “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema.
“Al comienzo de cada mes, presentarán al Señor un holocausto de dos novillos, un carnero y siete corderos machos de un año, todos ellos sin defectos,
12 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta;
junto con ofrendas de grano que consisten en tres décimas de una efa de la mejor harina mezclada con aceite de oliva para cada toro, dos décimas de una efa de la mejor harina mezclada con aceite de oliva para el carnero,
13 ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova.
y una décima de una efa de la mejor harina mezclada con aceite de oliva para cada uno de los corderos. Este es un holocausto aceptable para el Señor.
14 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka.
“Sus respectivas libaciones serán medio hin de vino por cada toro, un tercio de hin por el carnero y un cuarto de hin por cada cordero. Este es el holocausto mensual que se presentará cada mes durante el año.
15 Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.
Además del holocausto continuo con su libación, presentar un macho cabrío al Señor como ofrenda por el pecado.
16 “‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova.
“La Pascua del Señor es el día catorce del primer mes.
17 Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri.
Habrá una fiesta a los quince días de este mes, y durante siete días sólo se comerá pan sin levadura.
18 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Celebrarán una reunión sagrada el primer día de la fiesta. No hagan ninguna actividad de su trabajo normal.
19 Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema.
Preséntense ante el Señor con las siguientes ofrendas: un holocausto de dos novillos, un carnero y siete corderos de un año, todos ellos sin defectos.
20 Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse.
Sus ofrendas de grano se harán con la mejor harina mezclada con aceite de oliva: tres décimas de efa para cada toro, dos décimas de efa para el carnero,
21 Kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa asanu ndi awiri aja.
y una décima de efa para cada uno de los siete corderos.
22 Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu.
Presenten también una cabra macho como ofrenda por el pecado para hacerte justicia.
23 Muzikonza zimenezi nthawi zonse, powonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa.
Deben presentar estas ofrendas además del continuo holocausto de la mañana.
24 Motere muzikonza chakudya cha nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pa masiku asanu ndi awiri ngati fungo lokomera Yehova. Zimenezi ziziperekedwa kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse pamodzi ndi nsembe yachakumwa.
Presenta las mismas ofrendas todos los días durante siete días como holocausto para ser aceptado por el Señor. Deben ser ofrecidas con su libación y el continuo holocausto.
25 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Celebren una reunión sagrada el séptimo día del festival. Ese día no harán su trabajo usual.
26 “‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa.
“Durante la celebración del Festival de las Semanas, celebrarán una reunión sagrada el día de las primicias cuando presenten una ofrenda de grano nuevo al Señor. No hagan ningún tipo de trabajo.
27 Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova.
Presenten un holocausto de dos novillos, un carnero y siete corderos de un año para ser aceptados por el Señor.
28 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri.
Deben ir acompañados de sus ofrendas de grano de la mejor harina mezclada con aceite de oliva: tres décimos de un efa para cada toro, dos décimos de un efa para el carnero,
29 Ndipo pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja, kilogalamu imodzi.
y un décimo de un efa para cada uno de los siete corderos.
30 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu.
Presenten también una cabra macho como ofrenda para que los justifique.
31 Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema.
Presenten estas ofrendas junto con sus libaciones además del holocausto continuo y su ofrenda de grano. Asegúrate de que los animales sacrificados no tengan defectos”.