< Numeri 25 >

1 Aisraeli akukhala ku Sitimu, anayamba kuchita chigololo ndi akazi a ku Mowabu,
當以色列人住在史廷的時候,民眾開始與摩阿布女子行淫。
2 amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo.
這些女子請民眾參與她們神祗的祭祀;民眾吃了供物,且朝拜了她們的神祗。
3 Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri.
這樣以色列人就歸依了巴耳培敖爾,上主因此對以色列大發憤怒。
4 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga atsogoleri onse a anthu awa, uwaphe poyera, pamaso pa Yehova kuti mkwiyo waukulu wa Yehova uchoke pa Israeli.”
上主對梅瑟說:「你捉住民眾中所有的罪魁,在光天化日之下,為上主對他們懸掛起來,好挽回上主對以色列的怒火」。
5 Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.”
梅瑟就吩咐以色列的各首長說:「你們每人應將自已家中歸依巴耳培敖爾的人殺死」。
6 Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano.
看,當梅瑟和以色列子民全會眾都在會幕門口流淚痛哭時,以色列子民中正有一人,當他們的面,帶了一個米德揚女人到他兄弟那裏去。
7 Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni ataona izi, anachoka pa msonkhanowo, natenga mkondo mʼdzanja lake.
大司祭亞郎的兒子厄肋阿匝爾的兒子丕乃哈斯一見,就由會眾中起來,順手拿了一把長槍,
8 Ndipo anatsatira Mwisraeliyu mpaka mʼtenti yake. Anasolola mkondowo ndi kubaya awiriwo kupyola Mwisraeliyo mpaka mʼthupi la mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa Aisraeli.
跟那以色列人進入臥室內,刺穿了他們兩人,即那以色列和那女人的肚腹;以色列子民間的災禍遂止息了。
9 Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa.
在這次災禍內,死去了二萬四千人。
10 Yehova anawuza Mose kuti,
上主於是訓示梅瑟說:
11 “Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga.
「大司祭亞郎的孫子,厄肋阿匝爾床的丕乃哈斯,由以色列子民身上挽回了我的憤怒,因為他在他們中,懷著與我同樣的嫉邪的心,因此我沒有因我嫉邪之心消滅了以色列子民。
12 Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye.
為此你應聲明:看,我與他結平安的盟約。
13 Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli.”
這為他和他的後裔,是永享司祭品位的盟約,因為他為了自己天主的緣故,嫉惡如仇,賠補了以色列子民的罪」。
14 Dzina la Mwisraeli yemwe anaphedwa ndi mkazi wa Chimidiyani anali Zimuri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la Simeoni.
那與米德揚女人一同被殺的人,名叫齊默黎,是撒路的兒子,西滿盎家族的族長。
15 Ndipo dzina la mkazi wa Chimidiyani, yemwe anaphedwayo, linali Kozibi mwana wa Zuri, mtsogoleri wa fuko la ku Midiyaniko.
那被殺的米德揚女人,名叫苛次彼,是族爾的女兒;族爾是米德揚一部落的酋長。
16 Yehova anawuza Mose kuti,
事後,上主訓示梅瑟說:
17 “Amidiyani ndi adani anu ndipo uwaphe,
「你應2圍攻米德揚人,打擊他們,因為他們用詭計打擊了你們,就是在培敖爾的事上,
18 chifukwa ankakuonani inu ngati adani awo pamene anakupusitsani pa nkhani ya ku Peori, ndiponso za mlongo wawo Kozibi, mwana wamkazi wa mtsogoleri wa Amidiyani, mkazi yemwe anaphedwa pamene mliri unabwera chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”
並且他們的姊妹.米德揚酋長的女兒苛次彼的事上,欺騙了你們。──這女子已在培敖爾的事上,在災禍之日被殺」。

< Numeri 25 >