< Numeri 24 >
1 Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu.
2 Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye
3 ndipo ananena uthenga wake: “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,
4 uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:
5 “Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo, misasa yako, iwe Israeli!
6 “Monga zigwa zotambalala, monga minda mʼmbali mwa mtsinje, monga aloe wodzalidwa ndi Yehova, monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.
7 Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake; mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri. “Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi; ufumu wake udzakwezedwa.
8 “Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto ali ndi mphamvu ngati za njati. Amawononga mitundu yomuwukira ndi kuphwanya mafupa awo, amalasa ndi mivi yake.
9 Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi, monga mkango waukazi, adzamuputa ndani? “Amene adalitsa iwe, adalitsike ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”
10 Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka.
11 Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”
12 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine,
13 kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena?
14 Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”
15 Ndipo iye ananena uthenga wake nati, “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.
16 Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba, amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:
17 “Ndikumuona iye koma osati tsopano; ndikumupenya iye koma osati pafupi. Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo; ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli. Iye adzagonjetsa Mowabu ndi kugonjetsa ana onse a Seti.
18 Edomu adzagonjetsedwa; Seiri, mdani wake, adzawonongedwa koma mphamvu za Israeli zidzachuluka.
19 Wolamulira adzachokera mwa Yakobo ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.”
20 Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu: “Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu koma potsiriza pake adzawonongeka.”
21 Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake, “Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa, chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe;
22 komabe inu Akeni mudzawonongedwa, pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.”
23 Ndipo ananenanso uthenga wina kuti, “Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi?
24 Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu; kupondereza Asuri ndi Eberi, koma iwonso adzawonongeka.”
25 Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake.